Add parallel Print Page Options

10 Ndipo Samueli anatenga botolo la mafuta nathira mafutawo pa mutu wa Sauli ndipo anapsompsona nati, “Yehova wakudzoza kuti ukhale mtsogoleri wa anthu ake, Aisraeli. Iwe udzalamulira anthu a Yehova ndiponso udzawapulumutsa mʼmanja mwa adani awo owazungulira. Chizindikiro chakuti Yehova wakudzoza kuti ukhale mtsogoleri wa anthu ake ndi ichi: Ukachoka pano lero lino, udzakumana ndi amuna awiri kufupi ndi manda a Rakele ku Zeliza mʼmalire mwa dziko la Benjamini ndipo adzakuwuza kuti, ‘Abulu amene munkafunafuna aja apezeka. Ndipo tsopano abambo ako asiya kuganiza za abulu ndipo akudera nkhawa za iwe.’ Iwo akufunsa kuti, ‘Kodi ndidzachita chiyani mmene mwana wanga sakuoneka?’ ”

“Ndipo udzapyola pamenepo ndi kufika ku mtengo wa thundu wa ku Tabori. Kumeneko udzakumana ndi anthu atatu akupita kukapereka nsembe ku Nyumba ya Mulungu ku Beteli. Mmodzi adzakhala atanyamula ana ambuzi atatu, wina atanyamula malofu atatu a buledi, ndi winayo atanyamula thumba la vinyo. Adzakupatsa moni ndi kukupatsa malofu awiri a buledi. Iwe udzalandire bulediyo.

“Pambuyo pake, udzafike ku Gibeyati-Elohimu, kumene kuli gulu la ankhondo la Afilisti. Pamene ukuyandikira mzindawo, udzakumana ndi gulu la aneneri akutsika kuchokera ku phiri, akuyimba zeze, ngʼoma, zitoliro ndi pangwe, ndiponso akulosera. Kenaka Mzimu wa Yehova udzabwera pa iwe ndi mphamvu, ndipo udzayamba kulosera nawo pamodzi. Ndipo udzasinthika kukhala munthu wina. Zizindikiro izi zikakachitika, dzachite chilichonse manja ako angathe kuchita, pakuti Mulungu ali nawe.

“Tsono tsogola kupita ku Giligala. Ine ndidzabwera ndithu kudzapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano. Koma ukandidikire masiku asanu ndi awiri mpaka ine nditabwera kuti ndidzakuwuze zomwe udzachite.”

Sauli Avekedwa Ufumu

Sauli akutembenuka kusiyana ndi Samueli, Mulungu anasintha mtima wa Sauli, ndipo zinthu zonsezi zinakwaniritsidwa tsiku lomwelo. 10 Atafika ku Gibeya, anakumana ndi gulu la aneneri. Mzimu wa Mulungu unabwera pa iye mwamphamvu, nayamba kulosa nawo. 11 Pamene onse amene ankamudziwa kale anamuona akulosera pamodzi ndi aneneri, anafunsana wina ndi mnzake. “Kodi nʼchiyani chachitika ndi mwana wa Kisi? Kodi Sauli alinso mʼgulu la aneneri?”

12 Munthu wina wa kumeneko anayankha kuti, “Nanga enawa abambo awo ndani?” Kotero kunayambika mwambi wakuti, “Kodi Saulinso ali mʼgulu la aneneri?” 13 Sauli atasiya kuloserako, anapita ku kachisi ku phiri.

14 Tsono amalume ake a Sauli anamufunsa ndi mnyamata wake kuti, “Munapita kuti?”

Iye anayakha, “Timakafunafuna abulu koma titaona kuti sakupezeka, tinapita kwa Samueli.”

15 Amalume ake a Sauli anati, “Chonde, ndifotokozereniko zimene Samueli wakuwuzani.”

16 Sauli anati, “Iye anatitsimikizira kuti abulu anapezeka.” Koma sanawawuze amalume akewo za nkhani ija ya ufumu imene Samueli anamuwuza.

17 Samueli anayitana Aisraeli onse kuti asonkhane pamaso pa Yehova ku Mizipa. 18 Ndipo anawuza Aisraeli onse kuti, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ine ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto ndi kukupulumutsani mʼdzanja la Igupto ndi mʼdzanja la mafumu onse amene ankakuzunzani.’ 19 Koma lero mwamukana Mulungu wanu amene amakupulumutsani mʼmavuto anu onse ndi mʼzowawa zanu. Ndipo mukuti, ‘Ayi, koma mutipatse mfumu yotilamulira.’ Tsopanotu sonkhanani pamaso pa Yehova mwa mafuko ndi mabanja anu.”

20 Samueli atasonkhanitsa mafuko onse a Israeli, fuko la Benjamini linasankhidwa. 21 Anasonkhanitsa fuko la Benjamini banja ndi banja. Pomaliza anasonkhanitsa banja la Matiri mmodzimmodzi ndipo Sauli mwana wa Kisi anasankhidwa. Koma atamufunafuna, sanamupeze. 22 Tsono anthu anafunsanso kwa Yehova kuti, “Kodi munthuyu wabwera kale kuno?”

Ndipo Yehova anayankha kuti, “Inde wabisala pakati pa katundu.”

23 Iwo anathamanga ndi kukamutenga kumeneko. Atayimirira pakati pa anthu anapezeka kuti anali wamtali kuposa anthu ena mwakuti ankamulekeza mʼmapewa. 24 Samueli anafunsa anthu onse kuti, “Kodi mukumuona munthu amene Yehova wasankha? Palibe wofanana naye pakati pa anthu onse.”

Kenaka anthu onse anafuwula kuti, “Mfumu ikhale ndi moyo wautali!”

25 Samueli anafotokozera anthu ntchito ndi udindo wa mfumu. Pambuyo pake analemba mʼbuku zonse zokhudza ntchito ndi udindo wa mfumu, ndipo bukulo analiyika pamaso pa Yehova. Kenaka Samueli analola aliyense kuti abwerere kupita kwawo.

26 Sauli anapitanso ku mudzi kwawo ku Gibeya, pamodzi ndi anthu amphamvu amene Mulungu anawafewetsa mitima. 27 Koma anthu ena achabechabe anati, “Kodi munthu uyu angathe bwanji kutipulumutsa?” Iwo anayamba kumunyoza Sauliyo, ndipo sankamupatsa ngakhale mphatso. Koma iye sanalabadireko.

10 Then Samuel took a flask(A) of olive oil and poured it on Saul’s head and kissed him, saying, “Has not the Lord anointed(B) you ruler over his inheritance?[a](C) When you leave me today, you will meet two men near Rachel’s tomb,(D) at Zelzah on the border of Benjamin. They will say to you, ‘The donkeys(E) you set out to look for have been found. And now your father has stopped thinking about them and is worried(F) about you. He is asking, “What shall I do about my son?”’

“Then you will go on from there until you reach the great tree of Tabor. Three men going up to worship God at Bethel(G) will meet you there. One will be carrying three young goats, another three loaves of bread, and another a skin of wine. They will greet you and offer you two loaves of bread,(H) which you will accept from them.

“After that you will go to Gibeah(I) of God, where there is a Philistine outpost.(J) As you approach the town, you will meet a procession of prophets(K) coming down from the high place(L) with lyres, timbrels,(M) pipes(N) and harps(O) being played before them, and they will be prophesying.(P) The Spirit(Q) of the Lord will come powerfully upon you, and you will prophesy with them; and you will be changed(R) into a different person. Once these signs are fulfilled, do whatever(S) your hand(T) finds to do, for God is with(U) you.

“Go down ahead of me to Gilgal.(V) I will surely come down to you to sacrifice burnt offerings and fellowship offerings, but you must wait seven(W) days until I come to you and tell you what you are to do.”

Saul Made King

As Saul turned to leave Samuel, God changed(X) Saul’s heart, and all these signs(Y) were fulfilled(Z) that day. 10 When he and his servant arrived at Gibeah, a procession of prophets met him; the Spirit(AA) of God came powerfully upon him, and he joined in their prophesying.(AB) 11 When all those who had formerly known him saw him prophesying with the prophets, they asked each other, “What is this(AC) that has happened to the son of Kish? Is Saul also among the prophets?”(AD)

12 A man who lived there answered, “And who is their father?” So it became a saying: “Is Saul also among the prophets?”(AE) 13 After Saul stopped prophesying,(AF) he went to the high place.

14 Now Saul’s uncle(AG) asked him and his servant, “Where have you been?”

“Looking for the donkeys,(AH)” he said. “But when we saw they were not to be found, we went to Samuel.”

15 Saul’s uncle said, “Tell me what Samuel said to you.”

16 Saul replied, “He assured us that the donkeys(AI) had been found.” But he did not tell his uncle what Samuel had said about the kingship.

17 Samuel summoned the people of Israel to the Lord at Mizpah(AJ) 18 and said to them, “This is what the Lord, the God of Israel, says: ‘I brought Israel up out of Egypt, and I delivered you from the power of Egypt and all the kingdoms that oppressed(AK) you.’ 19 But you have now rejected(AL) your God, who saves(AM) you out of all your disasters and calamities. And you have said, ‘No, appoint a king(AN) over us.’(AO) So now present(AP) yourselves before the Lord by your tribes and clans.”

20 When Samuel had all Israel come forward by tribes, the tribe of Benjamin was taken by lot. 21 Then he brought forward the tribe of Benjamin, clan by clan, and Matri’s clan was taken.(AQ) Finally Saul son of Kish was taken. But when they looked for him, he was not to be found. 22 So they inquired(AR) further of the Lord, “Has the man come here yet?”

And the Lord said, “Yes, he has hidden himself among the supplies.”

23 They ran and brought him out, and as he stood among the people he was a head taller(AS) than any of the others. 24 Samuel said to all the people, “Do you see the man the Lord has chosen?(AT) There is no one like(AU) him among all the people.”

Then the people shouted, “Long live(AV) the king!”

25 Samuel explained(AW) to the people the rights and duties(AX) of kingship.(AY) He wrote them down on a scroll and deposited it before the Lord. Then Samuel dismissed the people to go to their own homes.

26 Saul also went to his home in Gibeah,(AZ) accompanied by valiant men(BA) whose hearts God had touched. 27 But some scoundrels(BB) said, “How can this fellow save us?” They despised him and brought him no gifts.(BC) But Saul kept silent.

Footnotes

  1. 1 Samuel 10:1 Hebrew; Septuagint and Vulgate over his people Israel? You will reign over the Lord’s people and save them from the power of their enemies round about. And this will be a sign to you that the Lord has anointed you ruler over his inheritance: