Add parallel Print Page Options

Hezekiya Mfumu ya Yuda

18 Mʼchaka chachitatu cha Hoseya mwana wa Ela mfumu ya Israeli, Hezekiya mwana wa Ahazi mfumu ya Yuda analowa ufumu. Anakhala mfumu ali ndi zaka 25 ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka 29. Amayi ake anali Abi, mwana wa Zekariya. Iye anachita zolungama pamaso pa Yehova monga anachitira Davide kholo lake. Anachotsa malo opembedzerako mafano, anaphwanya miyala yachipembedzo ndiponso anadula mafano a Asera. Iye anaphwanya njoka yamkuwa imene Mose anapanga, pakuti mpaka kufikira nthawi imeneyi Aisraeli amafukiza lubani kwa njoka imeneyi. (Imatchedwa Nehusitani).

Hezekiya anadalira Yehova Mulungu wa Israeli. Kotero panalibe wina wofanana naye pakati pa mafumu onse a Yuda, asanakhale mfumu kapena atakhala kale mfumu. Iye anakangamira Yehova ndipo sanamusiye koma anasunga malamulo amene Yehova anapatsa Mose. Ndipo Yehova anali naye ndipo kulikonse kumene anapita zinthu zinkamuyendera bwino. Iye anagalukira mfumu ya ku Asiriya ndipo sanayitumikirenso. Iye anakantha Afilisti kuyambira ku nsanja ya alonda mpaka ku mzinda wotetezedwa. Anakafika mpaka ku Gaza ndi ku malire ake.

Mʼchaka chachinayi cha Mfumu Hezekiya, chimene chinali chaka chachisanu ndi chiwiri cha Hoseya mwana wa Ela mfumu ya Israeli, Salimenezeri, mfumu ya ku Asiriya anabwera kudzathira nkhondo mzinda wa Samariya ndi kuwuzinga 10 Asiriya analanda mzindawu patatha zaka zitatu. Choncho mzinda wa Samariya unalandidwa chaka chachisanu ndi chimodzi cha Hezekiya, chimene chinali chaka chachisanu ndi chinayi cha Hoseya mfumu ya Israeli. 11 Mfumu ya ku Asiriya inatenga Aisraeli kupita nawo ku ukapolo ku Asiriya ndipo anakawakhazika ku Hala, ku Habori pafupi ndi mtsinje wa Gozani ndi mʼmizinda ya Amedi. 12 Izi zinachitika chifukwa sanamvere zonena za Yehova Mulungu wawo, koma anaphwanya pangano lake ndi zonse zimene Mose mtumiki wa Yehova anawalamula. Iwo sanamvere malamulowo kapena kuwagwiritsa ntchito.

13 Mʼchaka chakhumi ndi chinayi cha ulamuliro wa Mfumu Hezekiya, Senakeribu mfumu ya ku Asiriya anathira nkhondo mizinda yonse yotetezedwa ya Yuda, nayilanda. 14 Choncho Hezekiya mfumu ya Yuda anatumiza uthenga kwa mfumu ya ku Asiriya ku Lakisi wonena kuti, “Ine ndalakwa. Chokani kuno ndipo ndidzakupatsani chilichonse chimene munene.” Mfumu ya ku Asiriya inalamula mfumu Hezekiya, mfumu ya Yuda, kuti azipereka makilogalamu a siliva okwana 3,000 ndi makilogalamu a golide 1,000. 15 Mfumu Hezekiya inapereka siliva yense amene anapezeka mʼNyumba ya Yehova ndi mʼnyumba zosungiramo chuma cha mfumu.

16 Nthawi imeneyi Hezekiya mfumu ya Yuda anakanganula golide amene anakuta zitseko ndi mphuthu za chipata cha Nyumba ya Yehova namupereka kwa mfumu ya ku Asiriya.

Senakeribu Aopseza Yerusalemu

17 Mfumu ya ku Asiriya inatuma Taritani, Rabusarisi ndi Rabusake pamodzi ndi gulu lalikulu la ankhondo, kwa Mfumu Hezekiya ku Yerusalemu kuchokera ku Lakisi. Iwo anafika ku Yerusalemu nakayima pafupi ndi ngalande ya madzi yochokera ku Dziwe Lakumtunda, pa msewu waukulu wopita ku malo a Munda wa Mmisiri Wochapa. 18 Iwo anayitana mfumu, ndipo Eliyakimu mwana wa Hilikiya woyangʼanira nyumba ya mfumu, Sebina mlembi wa bwalo ndi Yowa mwana wa Asafu mlembi wa zochitika anapita kwa anthuwo.

19 Ndipo Rabusake anawawuza kuti, “Kamuwuzeni Hezekiya kuti,

“ ‘Mfumu yayikulu, mfumu ya ku Asiriya ikunena kuti, ‘Kodi chikukulimbitsa mtima ndi chiyani?’ 20 Iwe ukuti uli ndi luso ndiponso mphamvu pa nkhondo, komatu ukuyankhula mawu opanda pake. Kodi tsono iwe ukudalira yani kuti undiwukire ine? 21 Taona tsono, iwe ukudalira Igupto, bango lothyokalo, limene limalasa mʼmanja mwa munthu ngati waliyesa ndodo yoyendera! Umo ndi mmene Farao mfumu ya ku Igupto imachitira aliyense amene akuyidalira.’ ” 22 Ndipo ngati ukunena kwa ine kuti, “Ife tikudalira Yehova Mulungu wathu.” Kodi si Mulungu yemweyo amene nyumba zake ndi maguwa ake Hezekiya anachotsa, nawuza anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu kuti, “Muzipembedza pa guwa lansembe ili mu Yerusalemu?”

23 “ ‘Ndipo tsopano bwera udzakambirane ndi mbuye wanga, mfumu ya ku Asiriya: ine ndidzakupatsa akavalo 2,000 ngati ungathe kupeza okwerapo! 24 Ungathe bwanji kugonjetsa ngakhale mmodzi mwa akazembe angʼonoangʼono a mbuye wanga, pamene ukudalira Igupto kuti akupatse magaleta ndi anthu okwera pa akavalo? 25 Kuwonjezera pamenepa, kodi ine ndabwera kudzathira nkhondo ndi kuwononga malo ano popanda chilolezo cha Yehova? Yehova mwini ndiye anandiwuza kuti ndidzathire nkhondo ndi kuwononga dziko lino.’ ”

26 Pamenepo Eliyakimu mwana wa Hilikiya, Sebina ndi Yowa anawuza Rabusakeyo kuti, “Chonde yankhulani kwa atumiki anufe mʼChiaramu, popeza timachimva. Musayankhule nafe mu Chihebri kuopa kuti anthu onse amene ali pa khomapa angamve.”

27 Koma Rabusake anayankha kuti, “Kodi mbuye wanga wandituma kuti ndidzanene zinthu izi kwa mbuye wanu yekha ndi inu nokha basi? Ayi, komanso kwa anthu amene akhala pa khomawa. Iwowa adzadya chimbudzi chawo chomwe ndi kumwa mkodzo wawo womwe monga momwe mudzachitire inuyonso.”

28 Tsono Rabusake anayimirira nafuwula mu Chihebri kuti, “Imvani mawu a mfumu yayikulu, mfumu ya ku Asiriya! 29 Zimene mfumu ikunena ndi izi: ‘Musalole kuti Hezekiya akunamizeni. Iye sangakupulumutseni mʼdzanja langa. 30 Hezekiya asakukakamizeni kudalira Yehova ndi mawu akuti, ‘Ndithu, Yehova adzatipulumutsa; ndipo sadzapereka mzindawu mʼdzanja la mfumu ya ku Asiriya.’

31 “ ‘Musamumvere Hezekiya. Zimene mfumu ya ku Asiriya ikunena ndi izi: Pangani mtendere ndi ine ndipo mutuluke mu mzinda. Mukatero aliyense wa inu adzadya mphesa ndi nkhuyu za mʼmunda mwake ndiponso adzamwa madzi a mʼchitsime chake, 32 mpaka nditabwera kudzakutengani kupita ku dziko lofanana ndi lanuli, dziko la tirigu ndi vinyo watsopano, dziko la chakudya ndi minda ya mipesa, dziko la mitengo ya olivi ndi uchi. Sankhani moyo osati imfa!

“Musamvere zonena Hezekiya, pakuti iye akukusocheretsani ponena kuti, ‘Yehova adzatipulumutsa.’ 33 Kodi mulungu wa anthu a mtundu wina uliwonse wapulumutsapo dziko lake mʼdzanja la mfumu ya ku Asiriya? 34 Kodi ili kuti milungu ya Hamati ndi Aripadi? Ili kuti milungu ya Sefaravaimu, Hena ndi Ivani? Kodi inapulumutsa Samariya mʼdzanja langa? 35 Kodi ndi milungu iti mwa milungu yonse ya mayiko awa amene anapulumutsa dziko lake mʼdzanja langa? Nanga tsono Yehova adzapulumutsa Yerusalemu mʼdzanja langa motani?”

36 Koma anthu anakhala chete ndipo sanayankhepo kanthu, chifukwa mfumu inawalamula kuti, “Musayankhe.”

37 Pamenepo anthu atatu aja Eliyakimu, mwana wa Hilikiya amene ankayangʼanira nyumba ya mfumu, Sebina mlembi wa bwalo ndi Yowa mwana wa Asafu, mlembi wa zochitika anapita kwa Hezekiya atangʼamba zovala zawo ndipo anamuwuza Hezekiya zonse zimene anayankhula Rabusake uja.

Hezekiah King of Judah(A)(B)(C)

18 In the third year of Hoshea son of Elah king of Israel, Hezekiah(D) son of Ahaz king of Judah began to reign. He was twenty-five years old when he became king, and he reigned in Jerusalem twenty-nine years.(E) His mother’s name was Abijah[a] daughter of Zechariah. He did what was right(F) in the eyes of the Lord, just as his father David(G) had done. He removed(H) the high places,(I) smashed the sacred stones(J) and cut down the Asherah poles. He broke into pieces the bronze snake(K) Moses had made, for up to that time the Israelites had been burning incense to it. (It was called Nehushtan.[b])

Hezekiah trusted(L) in the Lord, the God of Israel. There was no one like him among all the kings of Judah, either before him or after him. He held fast(M) to the Lord and did not stop following him; he kept the commands the Lord had given Moses. And the Lord was with him; he was successful(N) in whatever he undertook. He rebelled(O) against the king of Assyria and did not serve him. From watchtower to fortified city,(P) he defeated the Philistines, as far as Gaza and its territory.

In King Hezekiah’s fourth year,(Q) which was the seventh year of Hoshea son of Elah king of Israel, Shalmaneser king of Assyria marched against Samaria and laid siege to it. 10 At the end of three years the Assyrians took it. So Samaria was captured in Hezekiah’s sixth year, which was the ninth year of Hoshea king of Israel. 11 The king(R) of Assyria deported Israel to Assyria and settled them in Halah, in Gozan on the Habor River and in towns of the Medes.(S) 12 This happened because they had not obeyed the Lord their God, but had violated his covenant(T)—all that Moses the servant of the Lord commanded.(U) They neither listened to the commands(V) nor carried them out.

13 In the fourteenth year(W) of King Hezekiah’s reign, Sennacherib king of Assyria attacked all the fortified cities of Judah(X) and captured them. 14 So Hezekiah king of Judah sent this message to the king of Assyria at Lachish:(Y) “I have done wrong.(Z) Withdraw from me, and I will pay whatever you demand of me.” The king of Assyria exacted from Hezekiah king of Judah three hundred talents[c] of silver and thirty talents[d] of gold. 15 So Hezekiah gave(AA) him all the silver that was found in the temple of the Lord and in the treasuries of the royal palace.

16 At this time Hezekiah king of Judah stripped off the gold with which he had covered the doors(AB) and doorposts of the temple of the Lord, and gave it to the king of Assyria.

Sennacherib Threatens Jerusalem(AC)(AD)

17 The king of Assyria sent his supreme commander,(AE) his chief officer and his field commander with a large army, from Lachish to King Hezekiah at Jerusalem. They came up to Jerusalem and stopped at the aqueduct of the Upper Pool,(AF) on the road to the Washerman’s Field. 18 They called for the king; and Eliakim(AG) son of Hilkiah the palace administrator, Shebna(AH) the secretary, and Joah son of Asaph the recorder went out to them.

19 The field commander said to them, “Tell Hezekiah:

“‘This is what the great king, the king of Assyria, says: On what are you basing this confidence(AI) of yours? 20 You say you have the counsel and the might for war—but you speak only empty words. On whom are you depending, that you rebel against me? 21 Look, I know you are depending on Egypt,(AJ) that splintered reed of a staff,(AK) which pierces the hand of anyone who leans on it! Such is Pharaoh king of Egypt to all who depend on him. 22 But if you say to me, “We are depending on the Lord our God”—isn’t he the one whose high places and altars Hezekiah removed, saying to Judah and Jerusalem, “You must worship before this altar in Jerusalem”?

23 “‘Come now, make a bargain with my master, the king of Assyria: I will give you two thousand horses—if you can put riders on them! 24 How can you repulse one officer(AL) of the least of my master’s officials, even though you are depending on Egypt for chariots and horsemen[e]? 25 Furthermore, have I come to attack and destroy this place without word from the Lord?(AM) The Lord himself told me to march against this country and destroy it.’”

26 Then Eliakim son of Hilkiah, and Shebna and Joah said to the field commander, “Please speak to your servants in Aramaic,(AN) since we understand it. Don’t speak to us in Hebrew in the hearing of the people on the wall.”

27 But the commander replied, “Was it only to your master and you that my master sent me to say these things, and not to the people sitting on the wall—who, like you, will have to eat their own excrement and drink their own urine?”

28 Then the commander stood and called out in Hebrew, “Hear the word of the great king, the king of Assyria! 29 This is what the king says: Do not let Hezekiah deceive(AO) you. He cannot deliver you from my hand. 30 Do not let Hezekiah persuade you to trust in the Lord when he says, ‘The Lord will surely deliver us; this city will not be given into the hand of the king of Assyria.’

31 “Do not listen to Hezekiah. This is what the king of Assyria says: Make peace with me and come out to me. Then each of you will eat fruit from your own vine and fig tree(AP) and drink water from your own cistern,(AQ) 32 until I come and take you to a land like your own—a land of grain and new wine, a land of bread and vineyards, a land of olive trees and honey. Choose life(AR) and not death!

“Do not listen to Hezekiah, for he is misleading you when he says, ‘The Lord will deliver us.’ 33 Has the god(AS) of any nation ever delivered his land from the hand of the king of Assyria? 34 Where are the gods of Hamath(AT) and Arpad?(AU) Where are the gods of Sepharvaim, Hena and Ivvah? Have they rescued Samaria from my hand? 35 Who of all the gods of these countries has been able to save his land from me? How then can the Lord deliver Jerusalem from my hand?”(AV)

36 But the people remained silent and said nothing in reply, because the king had commanded, “Do not answer him.”

37 Then Eliakim(AW) son of Hilkiah the palace administrator, Shebna the secretary, and Joah son of Asaph the recorder went to Hezekiah, with their clothes torn,(AX) and told him what the field commander had said.

Footnotes

  1. 2 Kings 18:2 Hebrew Abi, a variant of Abijah
  2. 2 Kings 18:4 Nehushtan sounds like the Hebrew for both bronze and snake.
  3. 2 Kings 18:14 That is, about 11 tons or about 10 metric tons
  4. 2 Kings 18:14 That is, about 1 ton or about 1 metric ton
  5. 2 Kings 18:24 Or charioteers