Add parallel Print Page Options

Salimo la Davide.

143 Yehova imvani pemphero langa,
    mvetserani kulira kwanga kopempha chifundo;
mwa kukhulupirika kwanu ndi chilungamo chanu
    bwerani kudzandithandiza.
Musazenge mlandu mtumiki wanu,
    pakuti palibe munthu wamoyo amene ndi wolungama pamaso panu.

Mdani akundithamangitsa,
    iye wandipondereza pansi;
wachititsa kuti ndikhale mu mdima
    ngati munthu amene anafa kale.
Choncho mzimu wanga ukufowoka mʼkati mwanga;
    mʼkati mwanga, mtima wanga uli ndi nkhawa.

Ndimakumbukira masiku amakedzana;
    ndimalingalira za ntchito yanu yonse,
    ndimaganizira zimene manja anu anachita.
Ndatambalitsa manja anga kwa Inu;
    moyo wanga uli ndi ludzu lofuna Inu monga nthaka yowuma.
            Sela

Yehova ndiyankheni msanga;
    mzimu wanga ukufowoka.
Musandibisire nkhope yanu,
    mwina ndidzakhala ngati iwo amene atsikira ku dzenje.
Lolani kuti mmawa ubweretse mawu achikondi chanu chosasinthika,
    pakuti ine ndimadalira Inu.
Mundisonyeze njira yoti ndiyendemo,
    pakuti kwa Inu nditukulira moyo wanga.
Pulumutseni kwa adani anga, Inu Yehova,
    pakuti ndimabisala mwa Inu.
10 Phunzitseni kuchita chifuniro chanu,
    popeza ndinu Mulungu wanga;
Mzimu wanu wabwino unditsogolere
    pa njira yanu yosalala.

11 Sungani moyo wanga Inu Yehova chifukwa cha dzina lanu;
    mwa chilungamo chanu tulutseni mʼmasautso anga.
12 Mwa chikondi chanu chosasinthika khalitsani chete adani anga;
    wonongani adani anga,
    pakuti ndine mtumiki wanu.