Add parallel Print Page Options

Gideoni

Aisraeli anachitanso zinthu zoyipira Yehova, choncho Yehova anawapereka mʼmanja mwa Amidiyani kwa zaka zisanu ndi ziwiri. Amidiyani anapondereza Aisraeli. Tsono chifukwa cha Amidiyaniwa, Aisraeli anakonza malo obisalamo mʼmapiri ndi mʼmapanga. Anamanganso malinga. Aisraeli amati akadzala mbewu, Amidiyani, Aamaleki ndi anthu ena akummawa amabwera ndi kudzawathira nkhondo. Iwo anamanga misasa mʼdzikomo ndi kuwononga zokolola zawo zonse mpaka ku Gaza, ndipo sanawasiyireko chamoyo chilichonse Aisraeliwo, kaya nkhosa kapena ngʼombe ndi bulu yemwe. Iwo ankabwera ndi zoweta zawo ndi matenti awo omwe. Ankabwera ambiri ngati dzombe, motero kuti kunali kovuta kuwawerenga anthuwo ndi ngamira zawo. Tsono iwo ankabwera ndi kuwononga dziko lonse. Aisraeli anasauka chifukwa cha Amidiyani ndipo analirira kwa Yehova kuti awathandize.

Pamene Aisraeli analirira kwa Yehova chifukwa cha Amidiyaniwo, Iye anawatumizira mneneri amene anati, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ndine amene ndinakutsogolerani kuchokera ku Igupto. Ndinakutulutsani mʼdziko la ukapolo. Ine ndinakupulumutsani ku ulamuliro wa Igupto komanso mʼmanja mwa amene amakuzunzani. Ndinawathamangitsa adani anu inu mukufika, ndikukupatsani dziko lawo.’ 10 Ndipo ndinakuwuzani kuti, ‘Ine ndine Yehova Mulungu wanu; musapembedze Milungu ya Aamori amene mukukhala mʼdziko lawo.’ Koma inu simunandimvere.”

11 Tsiku lina mngelo wa Yehova anabwera ku Ofura ndi kukhala pansi pa tsinde pa mtengo wa thundu umene unali wa Yowasi Mwabiezeri. Tsono Gideoni, mwana wake nʼkuti pa nthawiyo akupuntha tirigu mʼmalo ofinyira mphesa mowabisalira Amidiyani. 12 Tsono mngelo wa Yehova uja anamuonekera Gideoni nati kwa iye, “Yehova ali nawe, iwe munthu wamphamvu ndi wolimba mtima.”

13 Gideoni anayankha, “Koma mbuye wanga, ngati Yehova ali nafedi, nʼchifukwa chiyani zonsezi zationekera? Nanga ntchito zake zodabwitsa zimene makolo athu anatiwuza pamene anati, ‘Yehova anatitulutsa ku dziko la Igupto,’ zili kuti? Koma tsopano Yehova watitaya ndi kutipereka mʼmanja mwa Amidiyani.”

14 Yehova anamuyangʼana namuwuza kuti, “Pita ndi mphamvu zomwe uli nazo, ukapulumutse Aisraeli mʼmanja mwa Amidiyani. Kodi si ndine amene ndakutuma?”

15 Koma Gideoni anafunsa kuti, “Kodi Ambuye anga ine ndingapulumutse bwanji Israeli? Mbumba yanga ndi yopanda mphamvu mu fuko la Manase, ndiponso ine ndine wamngʼono kwambiri mʼbanja mwa abambo anga.”

16 Yehova anamuyankha kuti, “Ine ndidzakhala nawe, ndipo Amidiyaniwo udzawagonjetsa ngati munthu mmodzi.”

17 Gideoni anati, “Ngati tsopano mwandikomera mtima, ndionetseni chizindikiro kusonyeza kuti ndinudi mukuyankhula ndi ine. 18 Chonde musachoke msanga mpaka nditabwerera kwa inu ndi chopereka changa cha chakudya kudzachipereka kwa inu.”

Ndipo Yehova anamuwuza kuti, “Ine ndikudikira mpaka utabweranso.”

19 Gideoni analowa mʼnyumba, ndipo anakakonza mwana wambuzi, nakonzanso makeke wopanda yisiti a ufa wa makilogalamu khumi. Nayika nyamayo mʼdengu ndipo msuzi wake anawuthira mu mʼphika. Anabwera nazo ndi kukazipereka kwa mngelo uja pa tsinde pa mtengo wa thundu paja.

20 Mngelo wa Mulungu anamuwuza iye kuti, “Tenga nyamayi pamodzi ndi makekewa, uziyike pa mwala uwu ndi kuthirapo msuziwu.” Ndipo Gideoni anatero. 21 Mngelo wa Yehova anatenga msonga ya ndodo imene inali mʼmanja mwake nakhudza nayo nyama ndi makeke aja. Nthawi yomweyo moto unabuka pa thanthwepo ndi kupsereza nyama yonse ndi makeke aja. Ndipo mngelo wa Yehova sanaonekenso. 22 Apo Gideoni anazindikira kuti analidi mngelo wa Ambuye, ndipo anati, “Kalanga ine Yehova Wamphamvuzonse! Ine ndaona mngelo wa Yehova ndi maso!”

23 Koma Yehova anamuwuza kuti, “Mtendere ukhale ndi iwe! Usachite mantha, sufa ayi.”

24 Choncho Gideoni anamanga guwa lansembe la Yehova pamenepo ndipo analitcha kuti, Yehova ndiye mtendere. Kufikira lero lino guwali lilipo ku Ofura wa Mwabiezeri.

25 Usiku womwewo Yehova anati kwa Gideoni, “Tenga ngʼombe ya mphongo ya abambo ako, ngʼombe ina yachiwiri ya zaka zisanu ndi ziwiri ndipo ugwetse guwa la Baala limene abambo ako ali nalo, ndi kugwetsanso fano la Asera limene lili pafupi pake. 26 Kenaka umangire Yehova Mulungu wako guwa lansembe ndi miyala yoyala bwino pamwamba pa chiwunda chimenecho. Utenge ngʼombe ya mphongo yachiwiri ija ndipo uyipereke ngati nsembe yopsereza pogwiritsa ntchito mitengo ya fano la Asera imene udule ngati nkhunizo.”

27 Choncho Gideoni anatenga antchito ake khumi nachita monga Yehova anamuwuzira. Ndipo popeza ankaopa anthu a pa banja lake ndiponso anthu a mʼmudzimo sanachite zimenezi masana koma usiku.

28 Anthu a mu mzindamo atadzuka mʼmamawa anangoona guwa la Baala litagwetsedwa ndi fano la Asera limene linali pamwamba pake litadulidwa ndiponso ngʼombe yamphongo yachiwiri ija itaperekedwa ngati nsembe yopsereza pa guwa limene linamangidwa lija.

29 Iwo anafunsana wina ndi mnzake, “Wachita zimenezi ndani?”

Atafufuza ndi kufunsafunsa, analingalira kuti, “Gideoni mwana wa Yowasi ndiye wachita zimenezi.”

30 Ndipo anthuwo anawuza Yowasi kuti, “Tulutsa mwana wako, ayenera kufa chifukwa wagumula guwa lansembe la Baala ndipo wadula fano la Asera lomwe linali pamwamba pake.”

31 Koma Yowasi anawuza anthu amene anamuzungulirawo kuti, “Kodi inu mukuti mukhale woyankhulira Baala mlandu? Kodi ndinu amene mukuti mumupulumutse? Amene akufuna kumumenyera nkhondo Baala akhala atafa pofika mmawa! Ngati Baalayo ndi mulungudi, musiyeni adzimenyere yekha nkhondo popeza munthu wina wamugwetsera guwa lansembe lake.” 32 Choncho tsiku limenelo Gideoni anatchedwa, Yeru-Baala, kutanthauza kuti, “Baala alimbana naye, popeza anagwetsa guwa lake la nsembe.”

33 Tsopano Amidiyani, Amaleki ndi anthu ena akummawa anasonkhana ndipo atawoloka Yorodani anakamanga zinthando za nkhondo ku chigwa cha Yezireeli. 34 Ndipo Mzimu wa Yehova unatsikira pa Gideoni, ndipo anayimba lipenga kuyitana Abiezeri kuti amutsatire iye. 35 Iye anatumiza amithenga mʼdziko lonse la Manase kuti akamenye nkhondo ndipo Amanase anayitanidwanso kuti amutsate. Anatumanso amithenga kwa Aseri, Azebuloni ndi Anafutali, ndipo onsewo anapita kukakumana naye.

36 Gideoni anati kwa Mulungu, “Ngati mudzapulumutsa Israeli ndi dzanja langa monga mwalonjezeramu, 37 onani, ine ndiyala ubweya wankhosa pa malo opunthira tirigu. Ngati mame adzagwera pa ubweya wankhosa pokhapa, pa nthaka ponse pakhala powuma, ndiye ndidziwa kuti mudzapulumutsadi Israeli ndi dzanja langa monga mwanenera.” 38 Ndipo zimenezi zinachitikadi. Gideoni atadzuka mʼmamawa ndi kuwufinya ubweya uja, anafinya madzi odzaza mtsuko.

39 Kenaka Gideoni anati kwa Mulungu, “Musandikwiyire. Mundilole ndiyankhule kamodzi kokhaka. Ndiyeseko kamodzi kokha ndi ubweyawu kuti pa ubweya pokhapa pakhale powuma koma pa nthaka ponse pakhale ponyowa ndi mame.” 40 Ndipo Mulungu anachita zomwezo usiku umenewo. Pa ubweya pokha panali powuma, koma pa nthaka ponse panagwa mame.

Gideon

The Israelites did evil in the eyes of the Lord,(A) and for seven years he gave them into the hands of the Midianites.(B) Because the power of Midian was so oppressive,(C) the Israelites prepared shelters for themselves in mountain clefts, caves(D) and strongholds.(E) Whenever the Israelites planted their crops, the Midianites, Amalekites(F) and other eastern peoples(G) invaded the country. They camped on the land and ruined the crops(H) all the way to Gaza(I) and did not spare a living thing for Israel, neither sheep nor cattle nor donkeys. They came up with their livestock and their tents like swarms of locusts.(J) It was impossible to count them or their camels;(K) they invaded the land to ravage it. Midian so impoverished the Israelites that they cried out(L) to the Lord for help.

When the Israelites cried out(M) to the Lord because of Midian, he sent them a prophet,(N) who said, “This is what the Lord, the God of Israel, says: I brought you up out of Egypt,(O) out of the land of slavery.(P) I rescued you from the hand of the Egyptians. And I delivered you from the hand of all your oppressors;(Q) I drove them out before you and gave you their land.(R) 10 I said to you, ‘I am the Lord your God; do not worship(S) the gods of the Amorites,(T) in whose land you live.’ But you have not listened to me.”

11 The angel of the Lord(U) came and sat down under the oak in Ophrah(V) that belonged to Joash(W) the Abiezrite,(X) where his son Gideon(Y) was threshing(Z) wheat in a winepress(AA) to keep it from the Midianites. 12 When the angel of the Lord appeared to Gideon, he said, “The Lord is with you,(AB) mighty warrior.(AC)

13 “Pardon me, my lord,” Gideon replied, “but if the Lord is with us, why has all this happened to us? Where are all his wonders(AD) that our ancestors told(AE) us about when they said, ‘Did not the Lord bring us up out of Egypt?’ But now the Lord has abandoned(AF) us and given us into the hand of Midian.”

14 The Lord turned to him and said, “Go in the strength you have(AG) and save(AH) Israel out of Midian’s hand. Am I not sending you?”

15 “Pardon me, my lord,” Gideon replied, “but how can I save Israel? My clan(AI) is the weakest in Manasseh, and I am the least in my family.(AJ)

16 The Lord answered, “I will be with you(AK), and you will strike down all the Midianites, leaving none alive.”

17 Gideon replied, “If now I have found favor in your eyes, give me a sign(AL) that it is really you talking to me. 18 Please do not go away until I come back and bring my offering and set it before you.”

And the Lord said, “I will wait until you return.”

19 Gideon went inside, prepared a young goat,(AM) and from an ephah[a](AN) of flour he made bread without yeast. Putting the meat in a basket and its broth in a pot, he brought them out and offered them to him under the oak.(AO)

20 The angel of God said to him, “Take the meat and the unleavened bread, place them on this rock,(AP) and pour out the broth.” And Gideon did so. 21 Then the angel of the Lord touched the meat and the unleavened bread(AQ) with the tip of the staff(AR) that was in his hand. Fire flared from the rock, consuming the meat and the bread. And the angel of the Lord disappeared. 22 When Gideon realized(AS) that it was the angel of the Lord, he exclaimed, “Alas, Sovereign Lord! I have seen the angel of the Lord face to face!”(AT)

23 But the Lord said to him, “Peace! Do not be afraid.(AU) You are not going to die.”(AV)

24 So Gideon built an altar to the Lord there and called(AW) it The Lord Is Peace. To this day it stands in Ophrah(AX) of the Abiezrites.

25 That same night the Lord said to him, “Take the second bull from your father’s herd, the one seven years old.[b] Tear down your father’s altar to Baal and cut down the Asherah pole[c](AY) beside it. 26 Then build a proper kind of[d] altar to the Lord your God on the top of this height. Using the wood of the Asherah pole that you cut down, offer the second[e] bull as a burnt offering.(AZ)

27 So Gideon took ten of his servants and did as the Lord told him. But because he was afraid of his family and the townspeople, he did it at night rather than in the daytime.

28 In the morning when the people of the town got up, there was Baal’s altar,(BA) demolished, with the Asherah pole beside it cut down and the second bull sacrificed on the newly built altar!

29 They asked each other, “Who did this?”

When they carefully investigated, they were told, “Gideon son of Joash(BB) did it.”

30 The people of the town demanded of Joash, “Bring out your son. He must die, because he has broken down Baal’s altar(BC) and cut down the Asherah pole beside it.”

31 But Joash replied to the hostile crowd around him, “Are you going to plead Baal’s cause?(BD) Are you trying to save him? Whoever fights for him shall be put to death by morning! If Baal really is a god, he can defend himself when someone breaks down his altar.” 32 So because Gideon broke down Baal’s altar, they gave him the name Jerub-Baal[f](BE) that day, saying, “Let Baal contend with him.”

33 Now all the Midianites, Amalekites(BF) and other eastern peoples(BG) joined forces and crossed over the Jordan and camped in the Valley of Jezreel.(BH) 34 Then the Spirit of the Lord came on(BI) Gideon, and he blew a trumpet,(BJ) summoning the Abiezrites(BK) to follow him. 35 He sent messengers throughout Manasseh, calling them to arms, and also into Asher,(BL) Zebulun and Naphtali,(BM) so that they too went up to meet them.(BN)

36 Gideon said to God, “If you will save(BO) Israel by my hand as you have promised— 37 look, I will place a wool fleece(BP) on the threshing floor.(BQ) If there is dew only on the fleece and all the ground is dry, then I will know(BR) that you will save Israel by my hand, as you said.” 38 And that is what happened. Gideon rose early the next day; he squeezed the fleece and wrung out the dew—a bowlful of water.

39 Then Gideon said to God, “Do not be angry with me. Let me make just one more request.(BS) Allow me one more test with the fleece, but this time make the fleece dry and let the ground be covered with dew.” 40 That night God did so. Only the fleece was dry; all the ground was covered with dew.(BT)

Footnotes

  1. Judges 6:19 That is, probably about 36 pounds or about 16 kilograms
  2. Judges 6:25 Or Take a full-grown, mature bull from your father’s herd
  3. Judges 6:25 That is, a wooden symbol of the goddess Asherah; also in verses 26, 28 and 30
  4. Judges 6:26 Or build with layers of stone an
  5. Judges 6:26 Or full-grown; also in verse 28
  6. Judges 6:32 Jerub-Baal probably means let Baal contend.