Add parallel Print Page Options

Kulangidwa Kwa Babuloni

13 Uthenga onena za Babuloni umene Yesaya mwana wa Amozi anawulandira:

Kwezani mbendera yankhondo pa phiri loti see,
    muwafuwulire ankhondo;
muwakodole kuti adzalowe pa zipata
    za anthu olemekezeka.
Ine Yehova, ndalamulira ankhondo anga;
    ndasonkhanitsa ankhondo anga kuti akhale zida zanga zolangira
    amene amadzikuza ndi chipambano changa.

Tamvani phokoso ku mapiri,
    likumveka ngati phokoso la gulu lalikulu la anthu!
Tamvani phokoso pakati pa maufumu,
    ngati kuti mitundu ya anthu ikusonkhana pamodzi!
Yehova Wamphamvuzonse akukhazika asilikali ake mokonzekera
    kuchita nkhondo.
Iwo akuchokera ku mayiko akutali,
    kuchokera kumalekezero a dziko
Yehova ali ndi zida zake za nkhondo
    kuti adzawononge dziko la Babuloni.

Lirani mofuwula, pakuti tsiku la Yehova layandikira;
    lidzabwera ngati chiwonongeko chochokera kwa Wamphamvuzonse.
Zimenezi zinafowoketsa manja onse,
    mtima wa munthu aliyense udzachokamo.
Anthu adzagwidwa ndi mantha aakulu,
    zowawa ndi masautso zidzawagwera;
    adzamva zowawa zonga amamva mayi pobereka.
Adzayangʼanana mwamantha,
    nkhope zawo zikufiira ngati malawi amoto.

Taonani, tsiku la Yehova likubwera,
    tsiku lopanda chisoni, lawukali ndi lamkwiyo;
kudzasandutsa dziko kuti likhale chipululu
    ndi kuwononga anthu ochimwa a mʼmenemo.
10 Nyenyezi zakumwamba ndiponso zonse zamlengalenga
    sizidzaonetsa kuwala kwawo.
Dzuwa lidzada potuluka,
    ndipo mwezi sudzawala konse.
11 Ndidzalanga dziko lonse chifukwa cha zolakwa zake,
    anthu oyipa ndidzawalanga chifukwa cha machimo awo.
Ndidzathetsa kunyada kwa odzikuza,
    ndipo ndidzatsitsa kudzitukumula kwa anthu ankhanza.
12 Ndidzasandutsa anthu kukhala ovuta kupeza kuposa mmene amasowera golide wabwino.
    Iwo sazidzapezekapezeka kuposa mmene amasowera golide wa ku Ofiri.
13 Tsono ndidzagwedeza miyamba
    ndipo dziko lapansi lidzachoka pa maziko ake.
Izi zidzachitika chifukwa cha ukali wa Wamphamvuzonse
    pa tsiku la mkwiyo wake woopsa.

14 Ngati mbawala zosakidwa,
    ngati nkhosa zopanda wozikusa,
munthu aliyense adzabwerera kwa anthu akwawo,
    aliyense adzathawira ku dziko lake.
15 Aliyense amene atadzapezeke ndi kugwidwa
    adzaphedwa momubaya ndi lupanga.
16 Ana awo akhanda adzaphwanyidwa iwo akuona;
    nyumba zawo zidzafunkhidwa ndipo akazi awo adzagwiriridwa.

17 Taona, Ine ndidzadzutsa Amedi amene safuna siliva
    ndipo sasangalatsidwa ndi golide,
    kuti amenyane ndi Ababuloni.
18 Adzapha anyamata ndi mauta awo;
    sadzachitira chifundo ana
    ngakhale kumvera chisoni ana akhanda.
19 Babuloni, ufumu wake ndi waulemerero kuposa mafumu onse.
    Anthu ake amawunyadira.
Koma Yehova adzawuwononga
    ngati mmene anawonongera Sodomu ndi Gomora.
20 Anthu sadzakhalamonso
    kapena kukhazikikamo pa mibado yonse;
palibe Mwarabu amene adzayimike tenti yake,
    palibe mʼbusa amene adzawetamo ziweto zake.
21 Koma nyama zakuthengo ndizo zidzakhale kumeneko,
    nyumba zake zidzadzaza ndi nkhandwe;
mu mzindamo muzidzakhala akadzidzi,
    ndipo atonde akuthengo azidzalumphalumphamo.
22 Mu nsanja zake muzidzalira afisi,
    mʼnyumba zake zokongola muzidzalira nkhandwe.
Nthawi yake yayandikira
    ndipo masiku ake ali pafupi kutha.