Add parallel Print Page Options

Za Chilango cha Turo

23 Uthenga wonena za Turo:

Lirani mofuwula, inu oyendetsa sitima za pa madzi za ku Tarisisi:
    pakuti mzinda wa Turo wawonongedwa
    ndipo mulibe nyumba kapena dooko.
Zimenezi anazimva
    pochokera ku Kitimu.

Khalani chete inu anthu okhala mʼmbali mwa nyanja,
    inu amalonda a ku Sidoni,
    iwe amene unalemera ndi anthu oyenda pa nyanja.
Pa nyanja zazikulu
    panabwera tirigu wa ku Sihori;
zokolola za ku Nailo, ndipo munachita malonda
    ndi anthu a mitundu ina.

Chita manyazi, iwe Sidimu
    pakuti nyanja yayankhula, linga la ku nyanja (Turo) layankhula kuti,
“Sindinamvepo zowawa za kubereka kapena kuberekapo mwana;
    sindinalerepo ana aamuna kapena kulera ana aakazi.”
Mawuwa akadzamveka ku Igupto,
    iwo adzachita mantha akadzamva kuti Turo wawonongeka.

Wolokerani ku Tarisisi,
    lirani mofuwula, inu anthu okhala mʼmbali mwa nyanja.
Kodi uwu si mzinda wachisangalalo uja,
    mzinda wakalekale,
umene anthu ake ankapita
    kukakhala ku mayiko akutali?
Kodi ndani anakonza zimenezi kuti zigwere Turo, mzinda umene unakhazikitsa mizinda ina,
    mzinda umene amalonda ake ndi akalonga
ndi otchuka
    pa dziko lapansi?
Yehova Wamphamvuzonse anakonza zimenezi
    kuti athetse kunyada kwawo
    ndi kutsitsa anthu otchuka a pa dziko lapansi.

10 Mubalalike mʼdziko mwanu ngati mtsinje wa Nailo
    inu anthu a ku Tarisisi,
    pakuti mulibenso chokutetezani.
11 Yehova watambasula dzanja lake kuloza ku nyanja
    ndipo wagwedeza maufumu ake.
Iye walamula kuti Kanaani
    agwetse malinga ake.
12 Iye anati, “Simudzakondwanso konse,
    inu anthu opanikizidwa a ku Sidoni, tsopano wamphwanyidwa!

“Ngakhale muwolokere ku Kitimu,
    kumeneko simukapezako mpumulo.”
13 Onani dziko la Ababuloni,
    anthu amenewa tsopano atheratu!
Asiriya asandutsa Turo kukhala
    malo a zirombo za ku chipululu;
anamanga nsanja zawo za nkhondo,
    anagumula malinga ake
    ndipo anawasandutsa bwinja.

14 Lirani mofuwula, inu anthu oyendetsa sitima za pa madzi za ku Tarisisi;
    chifukwa malinga ako agwetsedwa!

15 Pa nthawi imeneyo Turo adzayiwalika pa zaka 70, amene ndi masiku a moyo wa mfumu. Koma potsiriza pa zaka 70 zimenezi, Turo adzakhala ngati mkazi wachiwerewere woyimbidwa mu nyimbo:

16 “Tenga zeze wako uzungulire mzinda,
    iwe mkazi wachiwerewere woyiwalika;
imba zeze mokometsera, imba nyimbo zambiri,
    kuti anthu akukumbukire.”

17 Pakutha pa zaka 70, Yehova adzachitapo kanthu pa Turo. Iye adzabwerera ku ntchito yake yakale monga mkazi wachiwerewere ndipo adzachita zachiwerewere ndi maufumu onse a dziko lapansi. 18 Koma phindu lake ndi malipiro ake adzazipereka kwa Yehova; sadzazikundika kapena kuzisunga. Phindu lake lidzapita kwa mtumiki wa Yehova kuti agule zakudya zambiri ndi zovala zokongola.