Add parallel Print Page Options

BUKU LOYAMBA

Masalimo 1–41

Wodala munthu
    amene satsatira uphungu wa anthu ochimwa,
kapena kuyima mʼnjira ya anthu oyipa,
    kapena kukhala mʼmagulu a anthu onyoza.
Koma chikondwerero chake chili mʼmalamulo a Yehova
    ndipo mʼmalamulo akewo amalingaliramo usana ndi usiku.
Iye ali ngati mtengo wodzalidwa mʼmbali mwa mitsinje ya madzi,
    umene umabereka zipatso zake pa nyengo yake
ndipo masamba ake safota.
    Chilichonse chimene amachita amapindula nacho.
Sizitero ndi anthu oyipa!
    Iwo ali ngati mungu
    umene umawuluzidwa ndi mphepo.
Kotero anthu oyipa sadzatha kuyima pa chiweruzo,
    kapena anthu ochimwa mu msonkhano wa anthu olungama.

Pakuti Yehova amayangʼanira mayendedwe a anthu olungama,
    koma mayendedwe a anthu oyipa adzawonongeka.
Nʼchifukwa chiyani anthu a mitundu ina akufuna kuchita chiwembu?
    Akonzekeranji zopanda pake anthu?
Mafumu a dziko lapansi akugwirizana nazo;
    ndipo olamulira asonkhana pamodzi
kulimbana ndi Ambuye
    ndi wodzozedwa wakeyo.
Iwo akunena kuti, “Tiyeni timasule magoli awo
    ndipo titaye zingwe zawo.”

Wokhala mmwamba akuseka;
    Ambuye akuwanyoza iwowo.
Ndipo iye awadzudzula mu mkwiyo wake
    ndi kuwaopseza mu ukali wake, kunena kuti,
“Ine ndakhazikitsa mfumu yanga
    pa Ziyoni, phiri langa loyera.”

Ine ndidzalengeza zimene Yehova walamula:

Iye anati kwa Ine, “Iwe ndiwe mwana wanga;
    lero Ine ndakhala Atate ako.
Tandipempha,
    ndipo ndidzachititsa kuti mitundu ya anthu ikhale cholowa chako;
    malekezero a dziko lapansi kuti akhale chuma chako.
Iweyo udzawalamulira ndi ndodo yaufumu yachitsulo;
    udzawaphwanya zidutswazidutswa ngati zowumba zadothi.”

10 Kotero, inu mafumu, chenjerani;
    chenjezedwani, inu olamulira a dziko lapansi.
11 Tumikirani Yehova mwa mantha
    ndi kukondwerera ulamuliro wake monjenjemera.
12 Mpsopsoneni mwanayo kuti angakwiye;
    kuti mungawonongedwe mʼnjira zanu,
pakuti ukali wake utha kuuka mʼkanthawi kochepa.
    Odala ndi onse amene amathawira kwa Iye.

Salimo la Davide. Atathawa mwana wake Abisalomu.

Inu Yehova, achulukadi adani anga!
    Achulukadi amene andiwukira!
Ambiri akunena za ine kuti,
    “Mulungu sadzamupulumutsa.”
            Sela

Koma Inu Yehova, ndinu chishango chonditeteza,
    Inu mwandiveka ulemerero ndipo mwanditukula.
Kwa Yehova, Ine ndilira mofuwula
    ndipo Iye amandiyankha kuchokera ku phiri lake loyera.
            Sela

Ine ndimagona ndi kupeza tulo;
    ndimadzukanso chifukwa Yehova amandichirikiza.
Sindidzaopa adani anga osawerengeka amene
    abwera kulimbana nane kuchokera ku madera onse.

Dzukani, Inu Yehova!
    Pulumutseni, Inu Mulungu wanga.
Akantheni adani anga onse pa msagwada;
    gululani mano a anthu oyipa.

Chipulumutso chimachokera kwa Yehova.
    Madalitso akhale pa anthu anu.
            Sela

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe wa zida za zingwe. Salimo la Davide.

Ndiyankheni pamene ndiyitana Inu,
    Inu Mulungu wa chilungamo changa.
Pumulitseni ku zowawa zanga;
    chitireni chifundo ndi kumva pemphero langa.

Anthu inu, mpaka liti mudzakhala mukusandutsa ulemerero wanga kukhala manyazi?
    Mpaka liti mudzakonda zachabe ndi kufuna milungu yabodza?
            Sela.
Dziwani kuti Yehova wadziyikira padera anthu okhulupirika;
    Yehova adzamva pamene ndidzamuyitana.

Kwiyani koma musachimwe;
    pamene muli pa mabedi anu,
    santhulani mitima yanu ndi kukhala chete.
            Sela
Perekani nsembe zolungama
    ndipo dalirani Yehova.

Ambiri akufunsa kuti, “Ndani angationetse chabwino chilichonse?”
    Kuwunika kwa nkhope yanu kutiwalire, Inu Yehova.
Inu mwadzaza mtima wanga ndi chimwemwe chachikulu
    kuposa kuchuluka kwa tirigu wawo ndi vinyo watsopano.
Ine ndidzagona ndi kupeza tulo mwamtendere,
    pakuti Inu nokha, Inu Yehova,
    mumandisamalira bwino.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe zoyimbira za zitoliro. Salimo la Davide.

Tcherani khutu ku mawu anga, Inu Yehova,
    ganizirani za kusisima kwanga
Mverani kulira kwanga kofuna thandizo,
    Mfumu yanga ndi Mulungu wanga,
    pakuti kwa Inu, ine ndikupemphera.
Mmawa, Yehova mumamva mawu anga;
    Mmawa ndimayala zopempha zanga pamaso panu
    ndi kudikira mwachiyembekezo.

Inu si Mulungu amene mumasangalala ndi zoyipa;
    choyipa sichikhala pamaso panu.
Onyada sangathe kuyima pamaso panu;
    Inu mumadana ndi onse ochita zoyipa.
Mumawononga iwo amene amanena mabodza;
    anthu akupha ndi achinyengo,
    Yehova amanyansidwa nawo.

Koma Ine, mwa chifundo chanu chachikulu,
    ndidzalowa mʼNyumba yanu;
mwa ulemu ndidzaweramira pansi
    kuyangʼana ku Nyumba yanu yoyera.
Tsogolereni Inu Yehova, mwa chilungamo chanu
    chifukwa cha adani anga ndipo
    wongolani njira yanu pamaso panga.

Palibe mawu ochokera mʼkamwa mwawo amene angadalirike;
    mtima wawo wadzaza ndi chiwonongeko.
Kummero kwawo kuli ngati manda apululu;
    ndi lilime lawo amayankhula zachinyengo.
10 Lengezani kuti ndi olakwa, Inu Mulungu!
    Zochita zawo zoyipa zikhale kugwa kwawo.
Achotseni pamaso panu chifukwa cha machimo awo ambiri,
    pakuti awukira Inu.

11 Koma lolani kuti onse amene apeza chitetezo mwa Inu akondwere;
    lolani kuti aziyimba nthawi zonse chifukwa cha chimwemwe.
Aphimbeni ndi chitetezo chanu,
    iwo amene amakonda dzina lanu akondwere mwa Inu.
12 Ndithu, Inu Yehova, mumadalitsa olungama;
    mumawazungulira ndi kukoma mtima kwanu ngati chishango.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za zingwe. Molingana ndi seminiti. Salimo la Davide.

Inu Yehova, musandidzudzule mu mkwiyo wanu,
    kapena kundilanga mu ukali wanu.
Ndichitireni chifundo Inu Yehova, pakuti ndalefuka;
    Inu Yehova chiritseni, pakuti mafupa anga ali pa ululu waukulu.
Moyo wanga uli pa mazunzo aakulu.
    Mpaka liti, Inu Yehova, mpaka liti?

Tembenukani Inu Yehova, ndipo mundilanditse;
    pulumutseni chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika.
Palibe amene amakukumbukirani pamene wamwalira;
    Amakutamandani ndani ali ku manda?

Ine ndatopa ndi kubuwula;
    usiku wonse pa bedi panga pamadzaza ndi misozi yanga;
    ndimanyowetsa pogona panga ndi misozi.
Maso anga atupa chifukwa cha chisoni;
    akulephera kuona chifukwa cha adani anga.

Chokani kwa ine inu nonse amene mumachita zoyipa,
    pakuti Yehova wamva kulira kwanga.
Yehova wamva kupempha kwanga kofuna chifundo;
    Yehova walandira pemphero langa.
10 Adani anga onse adzachita manyazi ndipo adzakhala ndi mantha;
    adzabwerera msangamsanga mwa manyazi.

Sigioni wa Davide, amene anayimbira Yehova zokhudza Kusi, wa fuko la Benjamini.

Inu Yehova Mulungu wanga, Ine ndikuthawira kwa Inu;
    pulumutseni ndi kundilanditsa kwa onse amene akundithamangitsa,
mwina angandikadzule ngati mkango,
    ndi kundingʼamba popanda wondipulumutsa.

Inu Yehova Mulungu wanga,
    ngati ndachita izi ndipo ndapezeka wolakwa,
ngati ndachita zoyipa kwa iye amene ndili naye pa mtendere,
    kapena popanda chifukwa ndalanda mdani wanga,
pamenepo lolani adani anga andithamangitse ndi kundipitirira,
    lolani kuti moyo wanga aupondereze pansi
    ndipo mundigoneke pa fumbi.
            Sela

Nyamukani Yehova, mu mkwiyo wanu;
    nyamukani kutsutsana ndi mkwiyo wa adani anga.
    Dzukani Mulungu wanga, lamulirani chilungamo chanu.
Lolani gulu la anthu a mitundu ina lisonkhane mokuzungulirani.
    Alamulireni muli kumwambako;
    Yehova aweruzeni anthu a mitundu inayo.
Ndiweruzeni Yehova, monga mwa chilungamo changa,
    monga mwa moyo wanga wangwiro, Inu Wammwambamwamba.
Inu Mulungu wolungama,
    amene mumasanthula maganizo ndi mitima,
thetsani chiwawa cha anthu oyipa
    ndipo wolungama akhale motetezedwa.

10 Chishango changa ndi Mulungu Wammwambamwamba,
    amene amapulumutsa olungama mtima.
11 Mulungu amaweruza molungama,
    Mulungu amene amaonetsa ukali wake tsiku ndi tsiku.
12 Ngati munthu satembenuka,
    Mulungu adzanola lupanga lake,
    Iye adzawerama ndi kukoka uta.
13 Mulungu wakonza zida zake zoopsa;
    Iye wakonzekera mivi yake yoyaka moto.

14 Taonani, munthu woyipa amalingalira zoyipa zokhazokha nthawi zonse.
    Zochita zake ndi zosokoneza ndi zovutitsa anthu ena.
15 Iye amene akumba dzenje ndi kulizamitsa
    amagwera mʼdzenje limene wakumbalo.
16 Mavuto amene amayambitsa amamubwerera mwini;
    chiwawa chake chimatsikira pa mutu wake womwe.

17 Ine ndidzayamika Yehova chifukwa cha chilungamo chake;
    ndipo ndidzayimba nyimbo zamatamando pa dzina la Yehova Wammwambamwamba.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa gititi. Salimo la Davide.

Inu Yehova Ambuye athu,
    dzina lanu ndi la lamphamvudi pa dziko lonse lapansi!

Inu mwakhazikitsa ulemerero wanu
    mʼmayiko onse akumwamba.
Kuchokera mʼkamwa mwa ana ndi makanda,
    Inu mwakhazikitsa mphamvu
chifukwa cha adani anu,
    kukhazikitsa bata adani ndi anthu obwezera zoyipa.

Pamene ndilingalira za mayiko anu akumwamba,
    ntchito ya zala zanu,
mwezi ndi nyenyezi,
    zimene mwaziyika pa malo ake,
munthu ndani kuti Inu mumamukumbukira,
    ndi mwana wa munthu kuti inu mumacheza naye?
Inu munamupanga kukhala wocheperapo kusiyana ndi zolengedwa zakumwamba
    ndipo mwamuveka ulemerero ndi ulemu.

Inu munamuyika wolamulira ntchito ya manja anu;
    munayika zinthu zonse pansi pa mapazi ake;
nkhosa, mbuzi ndi ngʼombe pamodzi
    ndi nyama zakuthengo,
mbalame zamlengalenga
    ndi nsomba zamʼnyanja
    zonse zimene zimayenda pansi pa nyanja.

Inu Yehova, Ambuye athu,
    dzina lanu ndi lamphamvudi pa dziko lonse lapansi!

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Monga mwa mayimbidwe a nyimbo ya “Imfa ya Mwana.” Salimo la Davide.

Ine ndidzakutamandani, Inu Yehova, ndi mtima wanga wonse;
    ndidzafotokoza za zodabwitsa zanu zonse.
Ndidzakondwa ndi kusangalala mwa inu;
    Ndidzayimba nyimbo zamatamando pa dzina lanu, Inu Wammwambamwamba.

Adani anga amathawa,
    iwo amapunthwa ndi kuwonongedwa pamaso panu.
Pakuti Inu mwatsimikiza za kulungama kwanga ndi mlandu wanga;
    Inu mwakhala pa mpando wanu waufumu, kuweruza mwachilungamo.
Mwadzudzula mitundu ya anthu ndipo mwawononga anthu oyipa;
    Inu mwafafaniza dzina lawo kwamuyaya.
Chiwonongeko chosatha chagwera adani,
    mwafafaniza mizinda yawo;
    ngakhale chikumbutso chawo chawonongedwa.

Yehova akulamulira kwamuyaya;
    wakhazikitsa mpando wake waufumu woweruzira.
Iye adzaweruza dziko mwachilungamo;
    adzalamulira mitundu ya anthu mosakondera.
Yehova ndiye kothawirako kwa opsinjika mtima,
    linga pa nthawi ya mavuto.
10 Iwo amene amadziwa dzina lanu adzadalira Inu,
    pakuti Inu Yehova, simunawatayepo amene amafunafuna inu.

11 Imbani nyimbo zamatamando kwa Yehova, ali pa mpando waufumu mu Ziyoni;
    lengezani pakati pa mitundu ya anthu zimene wachita.
12 Pakuti Iye amene amabwezera chilango akupha anzawo wakumbukira;
    Iye salekerera kulira kwa ozunzika.

13 Inu Yehova, onani momwe adani anga akundizunzira!
    Chitireni chifundo ndipo ndichotseni pa zipata za imfa,
14 kuti ndilengeze za matamando anu
    pa zipata za ana aakazi a Ziyoni,
    kuti pamenepo ndikondwere ndi chipulumutso chanu.
15 Mitundu ya anthu yagwa mʼdzenje limene yakumba;
    mapazi awo akodwa mu ukonde umene anawubisa.
16 Yehova amadziwika ndi chilungamo chake;
    oyipa akodwa ndi ntchito za manja awo.
            Higayoni. Sela
17 Oyipa amabwerera ku manda,
    mitundu yonse imene imayiwala Mulungu.
18 Koma osowa sadzayiwalika nthawi zonse,
    kapena chiyembekezo cha ozunzika kutayika nthawi zonse.

19 Dzukani Inu Yehova, musalole munthu kuti apambane;
    mitundu yonse iweruzidwe pamaso panu.
20 Akantheni ndi mantha aakulu, Inu Yehova;
    mitundu idziwe kuti iwo ndi anthu wamba.
            Sela
10 Nʼchifukwa chiyani Yehova mwayima patali?
    Chifukwa chiyani mukudzibisa nokha pa nthawi ya mavuto?

Mwa kunyada kwake munthu woyipa asaka wofowoka,
    amene akodwa mʼnjira zimene iye wakonza.
Iye amatamandira zokhumba za mu mtima wake;
    amadalitsa aumbombo ndi kuchitira chipongwe Yehova.
Mwa kunyada kwake woyipa safunafuna Mulungu;
    mʼmaganizo ake wonse mulibe malo a Mulungu.
Zinthu zake zimamuyendera bwino;
    iye ndi wamwano ndipo malamulo anu ali nawo kutali;
    amanyogodola adani ake onse.
Iye amadziyankhulira kuti, “Palibe chimene chidzandigwedeze.
    Ndidzakhala wokondwa nthawi zonse ndipo sindidzakhala pa mavuto.”
Mʼkamwa mwake mwadzaza matemberero, mabodza ndi zoopseza;
    zovutitsa ndi zoyipa zili pansi pa lilime lake.
Iye amabisalira anthu pafupi ndi midzi,
    kuchokera pobisalapo amapha anthu osalakwa,
    amayangʼanayangʼana mwachinsinsi anthu oti awawononge.
Amabisalira anthu ngati mkango pa zitsamba.
    Amabisalira kuti agwire anthu opanda mphamvu;
    amagwira anthu opanda mphamvu ndi kuwakokera mu ukonde wake.
10 Anthuwo amawapondaponda ndipo amakomoka;
    amakhala pansi pa mphamvu zake.
11 Iye amati mu mtima mwake, “Mulungu wayiwala,
    wabisa nkhope yake ndipo sakuonanso.”

12 Dzukani Yehova! Onetsani dzanja lanu Inu Mulungu.
    Musayiwale anthu opanda mphamvu.
13 Nʼchifukwa chiyani munthu woyipa amachitira chipongwe Mulungu?
    Chifukwa chiyani amati mu mtima mwake,
    “Iye sandiyimba mlandu?”
14 Komatu Inu Mulungu, mumazindikira mavuto ndi zosautsa,
    mumaganizira zochitapo kanthu.
Wovutikayo amadzipereka yekha kwa Inu pakuti
    Inu ndi mthandizi wa ana amasiye.
15 Thyolani dzanja la woyipitsitsa ndi la munthu woyipa;
    muzengeni mlandu chifukwa cha zoyipa zake
    zimene sizikanadziwika.

16 Yehova ndi Mfumu kwamuyaya;
    mitundu ya anthu idzawonongeka kuchoka mʼdziko lake.
17 Mumamva Inu Yehova, zokhumba za osautsidwa;
    mumawalimbikitsa ndipo mumamva kulira kwawo.
18 Kuteteza ana amasiye ndi oponderezedwa,
    ndi cholinga chakuti munthu amene ali wa dziko lapansi asaopsenso.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.

11 Mwa Yehova ine ndimathawiramo.
    Nanga mungathe bwanji kunena kwa ine kuti,
    “Thawira ku phiri lako ngati mbalame.
Pakuti taona oyipa akunga mauta awo;
    ayika bwino mivi yawo pa zingwe za uta,
pobisala pawo kuti alase
    olungama mtima.
Tsono ngati maziko awonongeka,
    olungama angachite chiyani?”

Yehova ali mʼNyumba yake yoyera;
    Yehova ali pa mpando wake waufumu kumwamba.
Iye amayangʼanitsitsa ana a anthu;
    maso ake amawayesa.
Yehova amayesa olungama,
    koma moyo wake umadana ndi oyipa,
    amene amakonda zachiwawa.
Iye adzakhuthulira pa oyipa
    makala amoto ndi sulufule woyaka;
    mphepo yotentha idzakhala yowayenera.

Pakuti Yehova ndi wolungama,
    Iye amakonda chilungamo;
    ndipo anthu olungama adzaona nkhope yake.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Monga mwa mayimbidwe seminiti. Salimo la Davide.

12 Thandizeni Yehova pakuti palibe munthu wokhulupirika;
    okhulupirika akusowa pakati pa anthu.
Aliyense amanamiza mʼbale wake;
    ndi pakamwa pawo pabodza amayankhula zachinyengo.

Inu Yehova tsekani milomo yonse yachinyengo
    ndi pakamwa paliponse podzikuza.
Pakamwa pamene pamati, “Ife tidzapambana ndi kuyankhula kwathu;
    pakamwapa ndi pathupathu, tsono mbuye wathu ndani?”

“Chifukwa cha kuponderezedwa kwa anthu opanda mphamvu
    ndi kubuwula kwa anthu osowa,
Ine ndidzauka tsopano,” akutero Yehova,
    “Ndidzawateteza kwa owazunza.”
Ndipo mawu a Yehova ndi angwiro
    monga siliva oyengedwa mʼngʼanjo yadothi,
    oyengedwa kasanu nʼkawiri.

Inu Yehova mudzatitchinjiriza ndipo
    mudzatiteteza kwa anthu otere kwamuyaya.
Oyipa amangoyendayenda ponseponse
    anthu akamayamikira zochita zawo.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.

13 Mpaka liti Yehova? Kodi mudzandiyiwala mpaka kalekale?
    Mpaka liti mudzandibisira nkhope yanu?
Ndidzalimbana ndi maganizo anga
    ndi kukhala ndi chisoni mu mtima mwanga tsiku lililonse mpaka liti?
    Mpaka liti adani anga adzandipambana?

Ndiyangʼaneni ndi kundiyankha, Inu Yehova Mulungu wanga.
    Walitsani maso anga kuti ndingafe;
mdani wanga adzati, “Ndamugonjetsa,”
    ndipo adani anga adzakondwera pamene ine ndagwa.

Koma ndikudalira chikondi chanu chosasinthika;
    mtima wanga umakondwera ndi chipulumutso chanu.
Ine ndidzayimbira Yehova
    pakuti wandichitira zokoma.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.

14 Chitsiru chimati mu mtima mwake,
    “Kulibe Mulungu.”
Oterewa ndi oyipa ndipo ntchito zawo ndi zonyansa;
    palibe amene amachita zabwino.

Yehova kumwamba wayangʼana pansi,
    kuyangʼana anthu onse
kuti aone ngati alipo wina wanzeru,
    amene amafunafuna Mulungu.
Onse atembenukira kumbali,
    onse pamodzi asanduka oyipa;
palibe amene amachita zabwino,
    palibiretu ndi mmodzi yemwe.

Kodi anthu ochita zoyipawa sadziwa chilichonse?
    Akudya anthu anga ngati chakudya chawo
    ndipo satamanda Yehova?
Awo ali apowo, agwidwa ndi mantha aakulu,
    pakuti Mulungu ali mʼgulu la olungama.
Inu ochita zoyipa mumalepheretsa chikonzero cha anthu osauka,
    koma Yehova ndiye pothawirapo pawo.

Ndithu, chipulumutso cha Israeli chidzachokera ku Ziyoni!
    Pamene Yehova abwezeretsa ufulu wa anthu ake,
    Yakobo akondwere ndipo Israeli asangalale!

Salimo la Davide.

15 Yehova, ndani angathe kukhala mʼmalo anu opatulika?
    Kodi ndani angathe kukhala mʼphiri lanu loyera?

Munthu wa makhalidwe abwino,
    amene amachita zolungama,
woyankhula choonadi chochokera mu mtima mwake,
    ndipo mʼkamwa mwake simutuluka mawu osinjirira,
amene sachitira choyipa mnansi wake
    kapena kufalitsa mbiri yoyipa ya munthu mnzake,
amene sapereka ulemu kwa munthu woyipa.
    Koma amalemekeza amene amaopa Yehova,
amene amakwaniritsa zomwe walonjeza
    ngakhale pamene zikumupweteka,
amene amakongoletsa ndalama zake popanda chiwongoladzanja
    ndipo salandira chiphuphu pofuna kutsutsa anthu osalakwa.

Iye amene amachita zinthu zimenezi
    sadzagwedezeka konse.

Mikitamu ya Davide.

16 Ndisungeni Inu Mulungu,
    pakuti ine ndimathawira kwa Inu.

Ndinati kwa Yehova, “Inu ndinu Ambuye anga;
    popanda Inu, ine ndilibe chinthu chinanso chabwino.”
Kunena za oyera mtima amene ali pa dziko,
    amenewa ndi olemekezeka, amene ndimakondwera nawo.
Anthu amene amathamangira kwa milungu ina
    mavuto awo adzachulukadi.
Ine sindidzathira nawo nsembe zawo zamagazi
    kapena kutchula mayina awo ndi pakamwa panga.

Yehova, Inu mwandipatsa cholowa changa ndi chikho changa;
    mwateteza kolimba gawo langa.
Malire a malo anga akhala pabwino;
    ndithudi, ine ndili cholowa chokondweretsa kwambiri.

Ine ndidzatamanda Yehova amene amandipatsa uphungu;
    ngakhale usiku mtima wanga umandilangiza.
Ndayika Yehova patsogolo panga nthawi zonse.
    Popeza Iyeyo ali kudzanja langa lamanja,
    sindidzagwedezeka.

Choncho mtima wanga ndi wosangalala ndipo pakamwa panga pakukondwera;
    thupi langanso lidzakhala pabwino,
10 chifukwa Inu simudzandisiya ku manda,
    simudzalola kuti woyera wanu avunde.
11 Inu mwandidziwitsa njira ya moyo;
    mudzandidzaza ndi chimwemwe pamaso panu,
    ndidzasangalala mpaka muyaya pa dzanja lanu lamanja.

Pemphero la Davide.

17 Imvani Inu Yehova pempho langa lachilungamo;
    mverani kulira kwanga.
Tcherani khutu kuti mumve pemphero langa
    popeza silikuchokera pakamwa pachinyengo.
Kusalakwa kwanga kuchokera kwa inu;
    maso anu aone chimene ndi cholungama.

Ngakhale Inu mutafufuza mtima wanga ndi kundisanthula usiku,
    ngakhale mutandiyesa, simudzapeza kanthu;
    Ine ndatsimikiza kuti pakamwa panga sipadzachimwa.
Kunena za ntchito za anthu,
    monga mwa mawu a pakamwa panu,
Ine ndadzisunga ndekha
    posatsata njira zachiwawa.
Mayendedwe anga akhazikika pa njira zanu;
    mapazi anga sanaterereke.

Ine ndikuyitana Inu, Mulungu wanga, pakuti mudzandiyankha;
    tcherani khutu lanu kwa ine ndipo mumve pemphero langa.
Onetsani kudabwitsa kwa chikondi chanu chachikulu,
    Inu amene mumapulumutsa ndi dzanja lanu lamanja
    iwo amene amathawira kwa inu kuchoka kwa adani awo.
Mundisunge ine ngati mwanadiso;
    mundibise mu mthunzi wa mapiko anu,
kuchoka kwa oyipa amene amandizinga ine,
    kuchoka kwa anthu amene ndi adani anga, amene andizungulira ine.

10 Iwo amatseka mitima yawo yopanda chifundo,
    ndi pakamwa pawo amayankhula modzitamandira.
11 Andisaka, tsopano andizungulira
    ndi maso awo atcheru, kuti andigwetse pansi.
12 Iwo ali ngati mkango wofuna nyama;
    ngati mkango waukulu wokhala mobisala.

13 Dzukani Yehova, mulimbane nawo ndipo muwagwetse pansi;
    landitseni kuchoka kwa oyipa ndi lupanga lanu.
14 Inu Yehova, pulumutseni ndi dzanja lanu kwa anthu otere,
    kwa anthu a dziko lino amene mphotho yawo ili mʼmoyo uno.

Inu mumaletsa njala kwa amene asangalatsidwa nanu;
    ana awo aamuna ali ndi zinthu zambiri,
    ndipo iwo amasunga chuma cha ana awo.
15 Ndipo ine mʼchilungamo ndidzaona nkhope yanu;
    pamene ndidzadzuka, ndidzakondwera kwambiri poonana nanu.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide mtumiki wa Yehova. Iye anayimbira Yehova nyimbo iyi pamene Yehovayo anamupulumutsa mʼdzanja la adani ake onse ndiponso mʼdzanja la Sauli.

18 Davide anati: Ine ndimakukondani Inu Yehova, mphamvu zanga.

Yehova ndiye thanthwe langa, chitetezo changa ndi mpulumutsi wanga;
    Mulungu wanga ndi thanthwe langa mʼmene ndimathawiramo.
    Chishango changa ndi ndodo yachipulumutso changa, ndi linga langa.
Ndimayitana Yehova amene ndi woyenera matamando,
    ndipo ndapulumutsidwa kwa adani anga.

Zingwe za imfa zinandizinga;
    mitsinje yothamanga yachiwonongeko inandiopsa kwambiri.
Anandimanga ndi zingwe za ku manda;
    misampha ya imfa inalimbana nane.
Mʼmasautso anga ndinapemphera kwa Yehova;
    ndinalirira kwa Mulungu wanga kuti andithandize.
Ali mʼNyumba yake, anamva mawu anga;
    kulira kwanga kunafika pamaso pake ndi mʼmakutu mwake.

Dziko lapansi linanjenjemera ndi kuchita chivomerezi,
    ndipo maziko a mapiri anagwedezeka;
    ananjenjemera chifukwa Iye anakwiya.
Mʼmphuno mwake munatuluka utsi;
    moto wonyeketsa unatuluka mʼkamwa mwake,
    makala amoto anali lawilawi mʼkamwa mwake.
Iye anangʼamba thambo natsika pansi;
    pansi pa mapazi ake panali mitambo yakuda.
10 Iye anakwera pa Kerubi ndi kuwuluka;
    nawuluka ndi mphepo mwaliwiro.
11 Iye anapanga mdima kukhala chofunda chake,
    chophimba chake chomuzungulira chinali mitambo yakuda ya mlengalenga.
12 Mʼkuwala kumene kunali pamaso pake munkachokera matalala,
    makala amoto ndi ziphaliwali zongʼanima.
13 Yehova anabangula kumwamba ngati bingu,
    mawu a Wammwambamwamba anamveka ponseponse.
14 Iye anaponya mivi yake nabalalitsa adani ake,
    ndi zingʼaningʼani zake anawagonjetsa.
15 Zigwa za mʼnyanja zinaonekera poyera;
    maziko a dziko lapansi anakhala poyera,
Yehova atabangula mwaukali,
    pamene mpweya wamphamvu unatuluka mʼmphuno mwanu.

16 Ali kumwamba, Iye anatambalitsa dzanja lake ndipo anandigwira;
    anandivuwula mʼmadzi ozama.
17 Anandipulumutsa kwa mdani wanga wamphamvu,
    adani anga, amene anali amphamvu kuposa ine.
18 Adaniwo analimbana nane pamene ndinali pa mavuto,
    koma Yehova anali thandizo langa.
19 Iye anandipititsa kumalo otakasuka;
    anandipulumutsa chifukwa amakondwera nane.

20 Yehova wandithandiza molingana ndi chilungamo changa;
    molingana ndi makhalidwe anga abwino, Iye wandipulumutsa.
21 Pakuti ine ndinatsata njira za Yehova;
    ndilibe mlandu wochoka pamaso Mulungu wanga.
22 Malamulo ake onse ali pamaso panga;
    sindinasiye malangizo ake.
23 Ndakhala moyo wosalakwa pamaso pake
    ndipo ndakhala ndi kupewa tchimo.
24 Yehova wandipatsa mphotho molingana ndi chilungamo changa,
    molingana ndi kuyera kwa manja anga pamaso pake.

25 Kwa wokhulupirika, Inu mumaonetsa kukhulupirika kwanu;
    kwa anthu amakhalidwe abwino, Inu mumaonetsanso makhalidwe abwino,
26 kwa woyera mtima, Inu mumaonetsa kuyera mtima kwanu,
    koma kwa achinyengo mumaonetsanso kunyansidwa nawo.
27 Inu mumapulumutsa anthu odzichepetsa,
    koma anthu amtima odzikuza mumawatsitsa.
28 Inu Yehova, sungani nyale yanga kuti iziyakabe;
    Mulungu wanga wasandutsa mdima wanga kukhala kuwunika.
29 Ndi thandizo lanu nditha kulimbana ndi gulu la ankhondo;
    ndi Mulungu wanga nditha kuchita zosatheka ndi munthu.

30 Kunena za Mulungu, zochita zake ndi zangwiro;
    mawu a Yehova alibe cholakwika.
Iye ndi chishango
    kwa onse amene amathawira kwa Iye.
31 Mulungu wina ndi uti wofanana nanu Yehova?
    Ndipo ndani amene ndi Thanthwe kupatula Mulungu wathu?
32 Ndi Mulungu amene anandipatsa mphamvu
    ndi kulungamitsa njira yanga.
33 Iye amasandutsa mapazi anga kukhala ngati ambawala yayikazi;
    Iye amandithandiza kuyimirira pamwamba pa mapiri.
34 Iye amaphunzitsa manja anga kuchita nkhondo;
    manja anga amatha kuthyola uta wachitsulo.
35 Inu mumandipatsa chishango chachipambano,
    ndipo dzanja lanu lamanja limandichirikiza;
    mumawerama pansi kundikuza.
36 Munakulitsa njira yoyendamo ine,
    kuti mapazi anga asaguluke.

37 Ndinathamangitsa adani anga ndi kuwapitirira;
    sindinabwerere mpaka atawonongedwa.
38 Ndinakantha adaniwo kotero kuti sanathenso kudzuka;
    anagwera pa mapazi anga.
39 Inu munandiveka ndi mphamvu yokachitira nkhondo,
    munachititsa kuti ndigonjetse adani anga.
40 Inu munachititsa adani anga kutembenuka, kuonetsa misana yawo pothawa,
    ndipo ine ndinawononga adani angawo.
41 Iwo anafuwula kupempha thandizo, koma panalibe ndi mmodzi yemwe owapulumutsa.
    Analirira kwa Yehova koma sanawayankhe.
42 Ine ndinawaperesa ngati fumbi lowuluka ndi mphepo.
    Ndinawapondaponda ngati matope a mʼmisewu.

43 Inu mwandipulumutsa mʼmanja mwa anthu;
    mwandisandutsa kukhala mtsogoleri wa anthu a mitundu ina.
    Anthu amene sindikuwadziwa ali pansi pa ulamuliro wanga.
44 Alendo amadzipereka okha pamaso panga;
    akangomva za ine amandigonjera.
45 Iwo onse anataya mtima;
    anatuluka mʼmalinga awo akunjenjemera.

46 Yehova ndi wamoyo! Litamandidwe Thanthwe langa!
    Akuzike Mulungu Mpulumutsi wanga!
47 Iye ndi Mulungu amene amabwezera chilango,
    amene amagonjetsa anthu a mitundu yonse amene ali pansi pa ulamuliro wanga,
48     amene amandipulumutsa mʼmanja mwa adani anga.
Inu munandikuza kuposa adani anga;
    munandilanditsa mʼmanja mwa anthu ankhanza.
49 Choncho ine ndidzakutamandani pakati pa anthu a mitundu ina, Inu Yehova;
    ndidzayimba nyimbo zotamanda dzina lanu.
50 Iye amapereka chipambano chachikulu kwa mfumu yake;
    amaonetsa chikondi chosasinthika kwa wodzozedwa wake,
    kwa Davide ndi zidzukulu zake kwamuyaya.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.

19 Zakumwamba zimalengeza za ulemerero wa Mulungu;
    thambo limalalikira ntchito za manja ake.
Tsiku ndi tsiku zimayankhula mawu ambiri,
    usiku ndi usiku zimaonetsa poyera nzeru.
Palibe kuyankhula, palibe mawu aliwonse;
    liwu lawo silimveka.
Koma uthenga wawo umapita pa dziko lonse lapansi,
    mawuwo amafika mpaka
kumalekezero a dziko lapansi.
    Dzuwa lili ngati mkwatibwi wobwera kuchokera ku nsanja yake,
    ngati katswiri wokondwerera kuthamanga pa mpikisano.
Limatuluka kuyambira mbali ina ya thambo
    ndi kuzungulira mpaka mbali inanso;
    palibe chinthu chotha kupewa kutentha kwake.

Lamulo la Yehova ndi langwiro,
    kutsitsimutsa moyo.
Maumboni a Yehova ndi odalirika,
    amapereka nzeru kwa wopanda nzeru.
Malangizo a Yehova ndi olungama,
    amapereka chimwemwe mu mtima.
Malamulo a Yehova ndi onyezimira,
    amapereka kuwala.
Kuopa Yehova ndiye chinthu changwiro,
    chimakhala mpaka muyaya.
Maweruzo a Yehova ndi owona
    ndipo onse ndi olungama;
10 ndi a mtengowapatali kuposa golide,
    kuposa golide weniweni;
ndi otsekemera kuposa uchi,
    kuposa uchi wochokera pa chisa chake.
11 Mtumiki wanu amachenjezedwa nawo;
    powasunga pali mphotho yayikulu.

12 Ndani angathe kudziwa zolakwa zake?
    Mundikhululukire zolakwa zanga zobisika.
13 Muteteze mtumiki wanunso ku machimo ochita akudziwa;
    iwo asandilamulire.
Kotero ndidzakhala wosalakwa,
    wopanda mlandu wa tchimo lalikulu.

14 Mawu a mʼkamwa mwanga ndi zolingalira za mu mtima mwanga
    zikhale zokondweretsa pamaso panu,
    Inu Yehova, Thanthwe langa ndi Mpulumutsi wanga.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.

20 Yehova akuyankhe pamene uli pa msautso;
    dzina la Mulungu wa Yakobo likuteteze.
Iye atumize thandizo kuchokera ku malo ake opatulika;
    akugwirizize kuchokera ku Ziyoni.
Iye akumbukire nsembe zako zonse
    ndipo alandire nsembe zako zopsereza.
            Sela
Akupatse chokhumba cha mtima wako
    ndipo akuthandize kuti zonse wakonza zichitike.
Ife tidzafuwula ndi chimwemwe pamene iwe wapambana
    ndipo tidzanyamula mbendera zathu mʼdzina la Mulungu wathu,
Yehova ayankhe zopempha zako zonse.

Tsopano ndadziwa kuti Yehova amapulumutsa wodzozedwa wake;
    Iye amamuyankha kuchokera kumwamba ku malo ake opatulika
    ndi mphamvu yopulumutsa ya dzanja lake lamanja.
Ena amadalira magaleta ndipo ena akavalo
    koma ife tidzadalira dzina la Yehova Mulungu wathu.
Iwo amagonjetsedwa ndi kugwa,
    koma ife timadzuka ndi kuyima chilili.

Inu Yehova, pulumutsani mfumu!
    Tiyankheni pamene tikuyitanani!

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.

21 Inu Yehova, mfumu ikusangalala mu mphamvu yanu,
    chimwemwe chake nʼchachikuludi pa kupambana kumene mumapereka!
Inu mwayipatsa zokhumba za mtima wake
    ndipo simunayimane zopempha za pa milomo yake.
            Sela
Inu munayilandira ndi madalitso ochuluka
    ndipo munayiveka chipewa chaufumu chagolide weniweni pa mutu wake.
Iye anakupemphani moyo, ndipo munamupatsa
    masiku ochuluka kwamuyaya.
Kudzera mʼzigonjetso zimene munapereka, ulemerero wake ndi waukulu;
    Inu mwapereka pa iyo ulemerero ndi ufumu.
Zoonadi Inu mwayipatsa madalitso amuyaya,
    Inu mwayipatsa chisangalalo ndi chimwemwe chimene chili pamaso panu.
Pakuti mfumu imadalira Yehova;
    kudzera mʼchikondi chake chosatha cha Wammwambamwamba,
    iyo sidzagwedezeka.

Dzanja lanu lidzayimitsa adani anu onse;
    dzanja lanu lamanja lidzagwira adani anu.
Pa nthawi ya kuonekera kwanu
    mudzawasandutsa ngʼanjo yamoto yotentha.
Mu ukali wake Yehova adzawameza,
    ndipo moto wake udzawatha.
10 Inu mudzawononga ana awo pa dziko lapansi,
    zidzukulu zawo pakati pa anthu.
11 Ngakhale iwo akukonzereni chiwembu mwa kuchenjera kwawo
    sadzapambana;
12 pakuti mudzawapirikitsa ndipo adzaonetsa misana yawo
    pamene mudzawaloza ndi mivi yanu.

13 Mukwezeke Inu Yehova mʼmphamvu yanu,
    ife tidzayimba nyimbo ndi kutamanda mphamvu yanu.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Monga mwa “Mbawala yayikazi ya Mmawa.” Salimo la Davide.

22 Mulungu wanga, Mulungu wanga, nʼchifukwa chiyani mwandisiya?
    Chifuwa chiyani simukundithandiza ndi pangʼono pomwe?
    Nʼchifukwa chiyani simukumva mawu a kudandaula kwanga?
Inu Mulungu wanga, ine ndimalira masana, koma simuyankha,
    usikunso, ndipo sindikhala chete.

Inu ndinu Woyera, wokhala pa mpando waufumu;
    ndinu matamando a Israeli.
Pa inu makolo athu anadalira;
    iwo anadalira ndipo Inu munawapulumutsa.
Analirira kwa inu ndipo munawapulumutsa.
    Iwo anakhulupirira Inu ndipo simunawakhumudwitse.

Koma ine ndine nyongolotsi osati munthu,
    wosekedwa ndi wonyozedwa ndi anthu onse.
Onse amene amandiona amandiseka;
    amandiyankhulira mawu achipongwe akupukusa mitu yawo kunena kuti
“Iyeyu amadalira Yehova,
    musiyeni Yehovayo amulanditse.
Musiyeni Yehova amupulumutse
    popeza amakondwera mwa Yehovayo.”

Komabe Inu ndinu amene munandibadwitsa, munanditulutsa mʼmimba mwa amayi anga.
    Munachititsa kuti ndizikudalirani
    ngakhale pa nthawi imene ndinkayamwa.
10 Chibadwire ine ndinaperekedwa kwa Inu;
    kuchokera mʼmimba mwa amayi anga Inu mwakhala muli Mulungu wanga.
11 Musakhale kutali ndi ine,
    pakuti mavuto ali pafupi
    ndipo palibe wina wondipulumutsa.

12 Ngʼombe zazimuna zandizungulira;
    ngʼombe zazimuna zamphamvu za ku Basani zandizinga.
13 Mikango yobangula pokadzula nyama,
    yatsekula kwambiri pakamwa pawo kulimbana nane.
14 Ine ndatayika pansi ngati madzi
    ndipo mafupa anga onse achoka mʼmalo mwake.
Mtima wanga wasanduka phula;
    wasungunuka mʼkati mwanga.
15 Mphamvu zanga zauma ngati phale,
    ndipo lilime langa lamamatira ku nsagwada;
    mwandigoneka mʼfumbi la imfa.
16 Agalu andizungulira;
    gulu la anthu oyipa landizinga.
    Alasa manja ndi mapazi anga.
17 Ine nditha kuwerenga mafupa anga onse;
    anthu amandiyangʼanitsitsa ndi kundidzuma.
18 Iwo agawana zovala zanga pakati pawo
    ndi kuchita maere pa zovala zangazo.

19 Koma Inu Yehova, musakhale kutali;
    Inu mphamvu yanga, bwerani msanga kuti mudzandithandize.
20 Pulumutsani moyo wanga ku lupanga,
    moyo wanga wopambanawu ku mphamvu ya agalu.
21 Ndilanditseni mʼkamwa mwa mikango;
    pulumutseni ku nyanga za njati.

22 Ine ndidzalengeza dzina lanu kwa abale anga;
    ndidzakutamandani mu msonkhano.
23 Inu amene mumaopa Yehova mutamandeni!
    Inu zidzukulu zonse za Yakobo, mulemekezeni!
    Muopeni mwaulemu, inu zidzukulu zonse za Israeli!
24 Pakuti Iye sanapeputse kapena kunyoza
    kuvutika kwa wosautsidwayo;
Iye sanabise nkhope yake kwa iye.
    Koma anamvera kulira kwake kofuna thandizo.

25 Ndidzakutamandani pa msonkhano waukulu chifukwa cha zimene mwandichitira.
    Ndidzakwaniritsa lonjezo langa pamaso pa amene amaopa Inu.
26 Osauka adzadya ndipo adzakhuta;
    iwo amene amafunafuna Yehova adzamutamanda.
    Mitima yanu ikhale ndi moyo mpaka muyaya!
27 Malekezero onse a dziko lapansi
    adzakumbukira Yehova ndi kutembenukira kwa Iye,
ndipo mabanja a mitundu ya anthu
    adzawerama pamaso pake,
28 pakuti ulamuliro ndi wake wa Yehova
    ndipo Iye amalamulira anthu a mitundu yonse.

29 Anthu olemera onse a dziko lapansi adzachita phwando ndi kulambira;
    onse amene amapita ku fumbi adzagwada pamaso pake;
    iwo amene sangathe kudzisunga okha ndi moyo.
30 Zidzukulu zamʼtsogolo zidzamutumikira Iye;
    mibado ya mʼtsogolo idzawuzidwa za Ambuye.
31 Iwo adzalengeza za chilungamo chake
    kwa anthu amene pano sanabadwe
    pakuti Iye wachita zimenezi.

Salimo la Davide.

23 Yehova ndiye mʼbusa wanga, sindidzasowa kanthu.
    Amandigoneka pa msipu wobiriwira,
amanditsogolera ku madzi akumwa abwino,
    amatsitsimutsa moyo wanga.
Amanditsogolera mʼnjira zachilungamo
    chifukwa cha dzina lake.
Ngakhale ndiyende
    mʼchigwa cha mdima wakuda bii,
sindidzaopa choyipa,
    pakuti Inu muli ndi ine;
chibonga chanu ndi ndodo yanu
    zimanditonthoza.

Mumandikonzera chakudya
    adani anga akuona.
Mumadzoza mutu wanga ndi mafuta;
    chikho changa chimasefukira.
Zoonadi, zokoma ndi chikondi chosasinthika zidzanditsata
    masiku onse a moyo wanga,
ndipo ndidzakhala mʼNyumba ya Yehova
    kwamuyaya.

Salimo la Davide.

24 Dziko lapansi ndi la Yehova ndi zonse zimene zili mʼmenemo,
    dziko ndi onse amene amakhala mʼmenemo;
pakuti Iye ndiye anayika maziko ake pa nyanja
    ndi kulikhazika pamwamba pa madzi.

Ndani angakwere phiri la Yehova?
    Ndani angathe kuyima pa malo ake opatulika?
Iye amene ali ndi mʼmanja moyera ndi mtima woyera,
    amene sapereka moyo wake kwa fano
    kapena kulumbira mwachinyengo.
Iyeyo adzalandira madalitso kwa Yehova
    ndipo Mulungu mpulumutsi wake adzagamula kuti alibe mlandu.
Umenewo ndiwo mʼbado wa amene amafunafuna Yehova;
    amene amafunafuna nkhope yanu, Inu Mulungu wa Yakobo.
            Sela

Tukulani mitu yanu inu zipata;
    tsekukani, inu zitseko zakalekalenu,
    kuti Mfumu yaulemerero ilowe.
Kodi Mfumu yaulemereroyo ndani?
    Yehova Wamphamvuzonse,
    Yehova ndiye wamphamvu pa nkhondo.
Tukulani mitu yanu, inu zipata;
    tsekukani, inu zitseko zakalekalenu,
    kuti Mfumu yaulemerero ilowe.
10 Kodi Mfumu yaulemereroyo ndani?
    Yehova Wamphamvuzonse,
    Iye ndiye Mfumu yaulemerero.
            Sela

Salimo la Davide.

25 Kwa Inu Yehova, ndipereka moyo wanga.
    Ndimadalira Inu Mulungu wanga.
Musalole kuti ndichite manyazi
    kapena kuti adani anga andipambane.
Aliyense amene amayembekezera kwa Ambuye
    sadzachititsidwa manyazi
koma achinyengo ndiwo adzachititsidwe manyazi
    ndipo sadzakhala ndi chodzitetezera.

Ndidziwitseni njira zanu Inu Yehova,
    phunzitseni mayendedwe anu;
tsogolereni mʼchoonadi chanu ndi kundiphunzitsa,
    pakuti Inu ndinu Mulungu mpulumutsi wanga,
    ndipo chiyembekezo changa chili mwa Inu tsiku lonse.
Kumbukirani Inu Yehova chifundo ndi chikondi chanu chachikulu,
    pakuti ndi zakalekale.
Musakumbukire machimo a ubwana wanga
    ndi makhalidwe anga owukira;
molingana ndi chikondi chanu ndikumbukireni ine,
    pakuti Inu Yehova ndinu wabwino.

Yehova ndi wabwino ndi wolungama;
    choncho Iye akulangiza ochimwa mʼnjira yake.
Amatsogolera odzichepetsa kuti achite zolungama
    ndipo amawaphunzitsa njira zake.
10 Njira zonse za Yehova ndi zachikondi ndi zokhulupirika
    kwa iwo amene amasunga zofuna za pangano lake.
11 Chifukwa cha dzina lanu, Inu Yehova,
    khululukireni mphulupulu zanga, ngakhale kuti ndi zochuluka.
12 Tsono ndani munthu amene amaopa Yehova?
    Yehova adzamulangiza njira yoti ayitsate.
13 Iye adzakhala pa ulemerero masiku ake onse,
    ndipo zidzukulu zake zidzalandira dziko ngati cholowa chawo.
14 Yehova amawulula chinsinsi chake kwa iwo amene amamuopa;
    amawulula pangano lake kwa iwowo.
15 Maso anga ali pa Yehova nthawi zonse,
    pakuti ndi Iye yekha amene adzawonjola mapazi anga mu msampha.

16 Tembenukirani kwa ine ndipo mundikomere mtima,
    pakuti ndili ndekhandekha ndipo ndikuzunzika.
17 Masautso a mu mtima mwanga achulukirachulukira;
    masuleni ku zowawa zanga.
18 Penyani mazunzo anga ndi zovuta zanga
    ndipo mufafanize machimo anga onse.
19 Onani mmene adani anga achulukira
    ndi momwe chidani chawo ndi ine chakulira.
20 Tetezani moyo wanga ndi kundilanditsa;
    musalole kuti ndichite manyazi,
    pakuti ndimathawira kwa Inu.
21 Kukhulupirika ndi kulungama kwanga kunditeteze,
    chifukwa chiyembekezo changa chili mwa Inu.

22 Wombolani Israeli Inu Mulungu,
    ku mavuto ake onse!

Salimo la Davide.

26 Weruzeni Inu Yehova
    pakuti ndakhala moyo wosalakwa.
Ndadalira Yehova
    popanda kugwedezeka.
Patseni mayeso, Inu Yehova ndipo ndiyeseni,
    santhulani mtima wanga ndi maganizo anga;
pakuti chikondi chanu chili pamaso panga nthawi zonse,
    ndipo ndimayenda mʼchoonadi chanu nthawi zonse.
Ine sindikhala pansi pamodzi ndi anthu achinyengo,
    kapena kufunsa nzeru kwa achiphamaso.
Ndimanyansidwa ndi msonkhano wa anthu ochita zoyipa
    ndipo ndimakana kukhala pansi pamodzi ndi oyipa.
Ndimasamba mʼmanja mwanga kuonetsa kusalakwa kwanga
    ndi kupita kukatumikira pa guwa lanu la nsembe, Inu Yehova,
kulengeza mofuwula za matamando anu
    ndi kuwuza onse za ntchito zanu zodabwitsa.
Ndimakonda Nyumba imene Inu Yehova mumakhalamo,
    malo amene ulemerero wanu umapezekako.

Musachotse moyo wanga pamodzi ndi ochimwa,
    moyo wanga pamodzi ndi anthu akupha anzawo,
10 amene mʼmanja mwawo muli ndondomeko zoyipa,
    dzanja lawo lamanja ladzaza ndi ziphuphu.
11 Koma ine ndimakhala moyo wosalakwa;
    mu msonkhano wa anthu anu ndidzatamanda Yehova.

12 Ndayima pa malo wopanda zovuta
    ndipo ndidzatamanda Yehova mu msonkhano waukulu.

Salimo la Davide.

27 Yehova ndiye kuwunika kwanga ndi chipulumutso changa;
    ndidzaopa yani?
Yehova ndi linga la moyo wanga;
    ndidzachita mantha ndi yani?
Pamene anthu oyipa abwera kudzalimbana nane
    kudzadya mnofu wanga,
pamene adani anga ndi achiwembu andithira nkhondo,
    iwo adzapunthwa ndi kugwa.
Ngakhale gulu lankhondo lindizinge,
    mtima wanga sudzaopa.
Ngakhale nkhondo itayambika kulimbana nane,
    ngakhale nthawi imeneyo, ine ndidzalimbika mtima.

Chinthu chimodzi chokha chimene ndipempha kwa Yehova,
    ichi ndi chimene ndidzachifunafuna:
kuti ndikhale mʼNyumba ya Yehova
    masiku onse a moyo wanga,
ndi kuyangʼana kukongola kwa Yehova,
    ndi kumufunafuna Iye mʼNyumba yake.
Pakuti pa tsiku la msautso
    Iye adzanditeteza mʼmalo ake okhalamo;
adzandibisa mʼkati mwa Nyumba yake
    ndi kukhazika ine pamwamba pa thanthwe.
Kotero mutu wanga udzakwezedwa
    kuposa adani anga amene andizungulira;
pa Nyumba yake ndidzapereka nsembe ndi mfuwu wachimwemwe;
    ndidzayimba nyimbo kwa Yehova.

Imvani mawu anga pamene ndiyitana Inu Yehova
    mundichitire chifundo ndipo mundiyankhe.
Mtima wanga ukuti kwa Inu, “Funafuna nkhope yake!”
    Nkhope yanu Yehova ndidzayifunafuna.
Musandibisire nkhope yanu,
    musamubweze mtumiki wanu mwamkwiyo;
    mwakhala muli thandizo langa.
Musandikane kapena kunditaya,
    Inu Mulungu Mpulumutsi wanga.
10 Ngakhale abambo ndi amayi anga anditaya
    Yehova adzandisamala.
11 Phunzitseni njira yanu Inu Yehova,
    munditsogolere mʼnjira yowongoka
    chifukwa cha ondizunza.
12 Musandipereke ku zokhumba za adani anga,
    pakuti mboni zambiri zauka kutsutsana nane
    ndipo zikundiopseza.

13 Ine ndikutsimikiza mtima za zimenezi;
    ndidzaona ubwino wa Yehova
    mʼdziko la anthu amoyo.
14 Dikirani pa Yehova;
    khalani anyonga ndipo limbani mtima
    nimudikire Yehova.

Salimo la Davide.

28 Kwa Inu ine ndiyitana, Yehova ndinu Thanthwe langa;
    musakhale osamva kwa ine.
Pakuti mukapitirira kukhala chete,
    ndidzakhala ngati iwo amene atsikira ku dzenje.
Imvani kupempha chifundo kwanga
    pomwe ndikuyitana kwa Inu kuti mundithandize,
pomwe ndikukweza manja anga
    kuloza ku malo anu oyeretsetsa.

Musandikokere kutali pamodzi ndi anthu oyipa,
    pamodzi ndi iwo amene amachita zoyipa,
amene amayankhula mwachikondi ndi anzawo
    koma akusunga chiwembu mʼmitima mwawo.
Muwabwezere chifukwa cha zochita zawo
    ndi ntchito zawo zoyipa;
abwezereni chifuwa cha zimene manja awo achita
    ndipo mubweretse pa iwo zimene zowayenera.
Popeza iwowo sakhudzidwa ndi ntchito za Yehova,
    ndi zimene manja ake anazichita,
Iye adzawakhadzula
    ndipo sadzawathandizanso.

Matamando apite kwa Yehova,
    popeza Iye wamva kupempha chifundo kwanga.
Yehova ndiye mphamvu yanga ndi chishango changa;
    mtima wanga umadalira Iye, ndipo Ine ndathandizidwa.
Mtima wanga umalumphalumpha chifukwa cha chimwemwe
    ndipo ndidzayamika Iye mʼnyimbo.

Yehova ndi mphamvu ya anthu ake,
    linga la chipulumutso kwa wodzozedwa wake.
Pulumutsani anthu anu ndipo mudalitse cholowa chanu;
    mukhale mʼbusa wawo ndipo muwakweze kwamuyaya.

Salimo la Davide.

29 Perekani kwa Yehova, inu anthu amphamvu,
    perekani kwa Yehova ulemerero ndi mphamvu.
Perekani kwa Yehova ulemerero woyenera dzina lake,
    pembedzani Yehova mwa kukongola kwa chiyero chake.

Liwu la Yehova lili pamwamba pa madzi;
    Mulungu waulemerero abangula,
    Yehova abangula pamwamba pa madzi amphamvu.
Liwu la Yehova ndi lamphamvu;
    liwu la Yehova ndi laulemerero.
Liwu la Yehova limathyola mikungudza;
    Yehova amathyolathyola mikungudza ya ku Lebanoni.
Iye amachititsa Lebanoni kulumphalumpha ngati mwana wangʼombe,
    Siriyoni ngati mwana wa njati:
Liwu la Yehova limakantha
    ngati kungʼanima kwa mphenzi.
Liwu la Yehova limagwedeza chipululu;
    Yehova amagwedeza chipululu cha Kadesi.
Liwu la Yehova limapindapinda mibawa
    ndi kuyeretsa nkhalango.
Ndipo mʼNyumba mwake onse amafuwula kuti, “Ulemerero!”

10 Yehova amakhala pamwamba pa madzi osefukira,
    Yehova ndiye mfumu kwamuyaya.
11 Yehova amapereka mphamvu kwa anthu ake;
    Yehova amadalitsa anthu ake ndi mtendere.

Salimo la Davide. Nyimbo yoyimba popereka Nyumba ya Mulungu.

30 Ndidzakukwezani Yehova,
    chifukwa mwanditulutsa kwakuya,
    ndipo simunalole kuti adani anga akondwere pa ine.
Inu Yehova Mulungu wanga ndinapempha kwa Inu thandizo
    ndipo Inu munandichiritsa.
Inu Yehova, munanditulutsa ku manda,
    munandisunga kuti ndisatsalire mʼdzenje.

Imbirani Yehova inu anthu ake okhulupirika;
    tamandani dzina lake loyera.
Pakuti mkwiyo wake umakhala kwa kanthawi
    koma kukoma mtima kwake ndi kwa moyo wonse;
utha kuchezera kulira usiku wonse,
    koma chimwemwe chimabwera mmawa.

Pamene ndinaona kuti ndili otetezedwa ndinati,
    “Sindidzagwedezekanso.”
Inu Yehova, pamene munandikomera mtima,
    munachititsa phiri langa kuyima chilili;
koma pamene munabisa nkhope yanu,
    ndinataya mtima.

Kwa Inu Yehova ndinayitana;
    kwa Ambuye ndinapempha chifundo;
“Kodi pali phindu lanji powonongeka kwanga
    ngati nditsikira ku dzenje?
Kodi fumbi lidzakutamandani Inu?
    Kodi lidzalengeza za kukhulupirika kwanu?
10 Imvani Yehova ndipo mundichitire chifundo;
    Yehova mukhale thandizo langa.”

11 Inu munasandutsa kulira kwanga kukhala kuvina;
    munachotsa chiguduli changa ndi kundiveka ndi chimwemwe,
12 kuti mtima wanga uthe kuyimbira Inu usakhale chete.
    Yehova Mulungu wanga, ndidzapereka kwa Inu mayamiko kwamuyaya.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.

31 Mwa Inu Yehova, ine ndimathawiramo;
    musalole nʼkomwe kuti ndichititsidwe manyazi;
    mundipulumutse chifukwa cha chilungamo chanu.
Tcherani khutu lanu kwa ine,
    bwerani msanga kudzandilanditsa;
mukhale thanthwe langa lothawirapo,
    linga lolimba kundipulumutsa ine.
Popeza Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa,
    chifukwa cha dzina lanu tsogolereni ndi kundiwongolera.
Ndimasuleni mu msampha umene anditchera
    pakuti ndinu pothawirapo panga.
Mʼmanja mwanu ndipereka mzimu wanga;
    womboleni Yehova Mulungu wachoonadi.

Koma ine ndimadana nawo amene amamamatira mafano achabechabe;
    ine ndimadalira Yehova.
Ndidzakondwa ndi kusangalala mʼchikondi chanu
    popeza Inu munaona masautso anga
    ndipo mumadziwa kuwawa kwa moyo wanga.
Inu simunandipereke kwa mdani
    koma mwayika mapazi anga pa malo otakasuka.

Mundichitire chifundo Inu Yehova pakuti ndili pa mavuto;
    maso anga akulefuka ndi chisoni,
    mʼmoyo mwanga ndi mʼthupi mwanga momwe mukupweteka.
10 Moyo wanga ukunyeka chifukwa cha kuwawidwa mtima
    ndi zaka zanga chifukwa cha kubuwula;
mphamvu zanga zatha chifuwa cha masautso,
    ndipo mafupa anga akulefuka.
11 Chifukwa cha adani anga onse,
    ndine wonyozeka kwambiri ndi anansi anga;
ndine chochititsa manyazi kwa abwenzi anga.
    Iwo amene amandiona mu msewu amandithawa.
12 Ine ndinayiwalika kwa iwo ngati kuti ndinamwalira;
    ndakhala ngati mʼphika wosweka.
13 Pakuti ine ndamva zonena zoyipa za anthu ambiri;
    zoopsa zandizungulira mbali zonse;
iwo akukonza chiwembu kuti alimbane nane,
    kuti atenge moyo wanga.

14 Koma ndikudalira Inu Yehova;
    ndikunena kuti, “Ndinu Mulungu wanga.”
15 Masiku anga ali mʼmanja mwanu;
    ndipulumutseni kwa adani anga
    ndi kwa iwo amene akundithamangitsa.
16 Walitsani nkhope yanu pa mtumiki wanu;
    pulumutseni mwa chikondi chanu chosatha.
17 Yehova musalole kuti ndichite manyazi,
    pakuti ndalirira kwa Inu;
koma oyipa achititsidwe manyazi
    ndipo agone chete mʼmanda.
18 Milomo yawo yabodzayo ikhale chete,
    pakuti chifukwa cha kunyada
    ayankhula modzikuza kutsutsana ndi wolungama.

19 Ndi waukulu ubwino wanu
    umene mwawasungira amene amakuopani,
umene mumapereka anthu akuona
    kwa iwo amene amathawira kwa Inu.
20 Mu mthunzi wa pamalo popezeka panu muwabisa,
    kuwateteza ku ziwembu za anthu;
mʼmalo anu okhalamo mumawateteza
    kwa anthu owatsutsa.

21 Matamando akhale kwa Yehova,
    pakuti anaonetsa chikondi chake chodabwitsa kwa ine
    pamene ndinali mu mzinda wozingidwa.
22 Ndili mʼnkhawa zanga ndinati,
    “Ine ndachotsedwa pamaso panu!”
Komabe Inu munamva kupempha chifundo kwanga
    pamene ndinapempha thandizo kwa Inu.

23 Kondani Yehova oyera mtima ake onse!
    Yehova amasunga wokhulupirika
    koma amalanga kwathunthu anthu odzikuza.
24 Khalani ndi nyonga ndipo limbani mtima,
    inu nonse amene mumayembekezera Yehova.

Salimo la Davide. Malangizo.

32 Ngodala munthu
    amene zolakwa zake zakhululukidwa;
    amene machimo ake aphimbidwa.
Ngodala munthu
    amene machimo ake Yehova sawawerengeranso pa iye
    ndipo mu mzimu mwake mulibe chinyengo.

Pamene ndinali chete,
    mafupa anga anakalamba
    chifukwa cha kubuwula kwanga tsiku lonse.
Pakuti usana ndi usiku
    dzanja lanu linandipsinja;
mphamvu zanga zinatha
    monga nthawi yotentha yachilimwe.
            Sela
Kotero ine ndinavomereza tchimo langa kwa Inu,
    sindinabise mphulupulu zanga.
Ndinati, “Ine ndidzawulula
    zolakwa zanga kwa Yehova,
ndipo Inu munandikhululukira
    mlandu wa machimo anga.”
            Sela

Choncho aliyense okhulupirika apemphere kwa Inuyo
    pomwe mukupezeka;
ndithu pamene madzi amphamvu auka,
    sadzamupeza.
Inu ndi malo anga obisala;
    muzinditeteza ku mavuto ndipo muzindizinga
    ndi nyimbo zachipulumutso.
            Sela

Ndidzakulangiza ndi kukuphunzitsa njira imene udzayendamo;
    ndidzakupatsa uphungu ndi kukuyangʼanira.
Usakhale ngati kavalo kapena bulu,
    zimene zilibe nzeru,
koma ziyenera kuwongoleredwa ndi zitsulo za mʼkamwa ndi pamutu,
    ukapanda kutero sizibwera kwa iwe.
10 Zowawa ndi zambiri za anthu oyipa
    koma chikondi chosatha cha Yehova
    chimamuzinga munthu amene amadalira Iye.

11 Kondwerani mwa Yehova inu olungama;
    imbani, inu nonse amene muli owongoka mtima!
33 Imbirani Yehova mokondwera Inu olungama,
    nʼkoyenera kuti owongoka mtima azitamanda Iyeyo.
Mutamandeni Yehova ndi pangwe;
    muyimbireni Iye nyimbo pa zeze wa zingwe khumi.
Muyimbireni nyimbo yatsopano;
    imbani mwaluso, ndipo fuwulani mwachimwemwe.

Pakuti mawu a Yehova ndi olungama ndi owona;
    Iye ndi wokhulupirika pa zonse zimene amachita.
Yehova amakonda chilungamo ndipo amaweruza molungama;
    dziko lapansi ladzaza ndi chikondi chake chosatha.

Ndi mawu a Yehova mayiko akumwamba anapangidwa,
    zolengedwa zake ndi mpweya wa mʼkamwa mwake.
Iye amasonkhanitsa pamodzi madzi a mʼnyanja mʼmitsuko;
    amayika zozama mʼnyumba zosungiramo.
Dziko lonse lapansi liope Yehova;
    anthu onse amulemekeze Iye.
Pakuti Iye anayankhula ndipo zinakhalapo;
    Iye analamulira ndipo zinakhazikika.
10 Yehova amalepheretsa chikonzero cha anthu a mitundu ina;
    Iye amaphwanya zolinga za anthu ambiri.
11 Koma chikonzero cha Yehova chimakhala mpaka muyaya,
    zolinga za mu mtima mwake pa mibado yonse.

12 Wodala mtundu wa anthu umene Mulungu wake ndi Yehova,
    anthu amene Iye anawasankha kukhala cholowa chake.
13 Kuchokera kumwamba Yehova amayangʼana pansi
    ndi kuona anthu onse;
14 kuchokera ku malo ake okhalako Iye amayangʼanira
    onse amene amakhala pa dziko lapansi.
15 Iye amene amapanga mitima ya onse,
    amaona zonse zimene akuchita.
16 Palibe mfumu imene imapulumutsidwa chifukwa cha kukula kwa gulu lake lankhondo;
    palibe msilikali amene amathawa ndi mphamvu zake zazikulu.
17 Kavalo ndi chiyembekezo cha chabechabe cha chipulumutso,
    ngakhale ali ndi mphamvu yayikulu sangathe kupulumutsa.
18 Koma maso a Yehova ali pa iwo amene amaopa Iye;
    amene chiyembekezo chawo chili mʼchikondi chake chosatha,
19 kuwawombola iwo ku imfa
    ndi kuwasunga ndi moyo nthawi ya njala.

20 Ife timadikira kwa Yehova mwachiyembekezo;
    Iye ndiye thandizo lathu ndi chishango chathu.
21 Mwa Iye mitima yathu imakondwera,
    pakuti ife timadalira dzina lake loyera.
22 Chikondi chanu chosatha
    chikhale pa ife Inu Yehova, pamene tikuyembekeza kwa Inu.

Salimo la Davide. Pamene iye ananyengezera misala pamaso pa Abimeleki, amene anamupirikitsa, iyeyo nʼkuchoka.

34 Ndidzayamika Yehova nthawi zonse;
    matamando ake adzakhala pa milomo yanga nthawi zonse.
Moyo wanga udzanyadira Yehova;
    anthu osautsidwa amve ndi kukondwera.
Lemekezani Yehova pamodzi ndi ine;
    tiyeni pamodzi tikuze dzina lake.

Ine ndinafunafuna Yehova ndipo Iye anandiyankha;
    anandilanditsa ku mantha anga onse.
Iwo amene amayangʼana kwa Iye, nkhope zawo zimanyezimira;
    nkhope zawo sizikhala zophimbidwa ndi manyazi.
Munthu wosauka uno anayitana, ndipo Yehova anamumva;
    Yehova anamupulumutsa ku mavuto ake onse.
Mngelo wa Yehova amatchinjiriza amene amakonda Iye
    ndi kuwalanditsa.

Lawani ndipo onani kuti Yehova ndi wabwino;
    wodala munthu amene amathawira kwa Iye.
Wopani Yehova inu oyera mtima ake,
    pakuti iwo amene amaopa Iye sasowa kanthu.
10 Mikango itha kulefuka ndi kumva njala
    koma iwo amene amafunafuna Yehova sasowa kanthu kalikonse kabwino.

11 Bwerani ana anga, mundimvere;
    ndidzakuphunzitsani kuopa Yehova.
12 Aliyense wa inu amene amakonda moyo wake
    ndi kukhumba kuti aone masiku abwino ambiri,
13 asunge lilime lake ku zoyipa
    ndi milomo yake kuti isayankhule zonama.
14 Tembenuka kuchoka ku zoyipa ndipo chita zabwino;
    funafuna mtendere ndi kuwulondola.

15 Maso a Yehova ali pa olungama
    ndipo makutu ake ali tcheru kumva kulira kwawo;
16 nkhope ya Yehova ikutsutsana ndi amene amachita zoyipa,
    kuwachotsa kuti asawakumbukirenso pa dziko lapansi.

17 Olungama amafuwula, ndipo Yehova amawamva;
    Iye amawalanditsa ku mavuto awo onse.
18 Yehova ali pafupi kwa osweka mtima
    ndipo amapulumutsa iwo amene asweka mu mzimu.

19 Munthu wolungama atha kukhala ndi mavuto ambiri,
    Koma Yehova amamulanditsa ku mavuto onsewo,
20 Iye amateteza mafupa ake onse,
    palibe limodzi la mafupawo limene lidzathyoledwa.

21 Choyipa chidzapha anthu oyipa;
    adani a olungama adzapezeka olakwa.
22 Yehova amawombola atumiki ake;
    aliyense amene amathawira kwa Iye sadzapezeka wolakwa.

Salimo la Davide.

35 Inu Yehova, mulimbane nawo amene akulimbana nane;
    mumenyane nawo amene akumenyana nane.
Tengani chishango ndi lihawo;
    dzukani ndipo bwerani mundithandize.
Tengani mkondo ndi nthungo,
    kulimbana ndi iwo amene akundithamangitsa.
Uzani moyo wanga kuti,
    “Ine ndine chipulumutso chako.”

Iwo amene akufunafuna moyo wanga
    anyozedwe ndi kuchita manyazi;
iwo amene akukonza kuti moyo wanga uwonongeke
    abwerere mʼmbuyo mochititsa mantha.
Akhale ngati mankhusu owuluka ndi mphepo
    pamene mngelo wa Yehova akuwapirikitsa.
Njira yawo ikhale ya mdima ndi yoterera
    pamene mngelo wa Yehova akuwathamangitsa.
Popeza ananditchera ukonde popanda chifukwa
    ndipo popanda chifukwa andikumbira dzenje,
chiwonongeko chiwapeza modzidzimutsa
    ukonde umene iwo abisa uwakole,
    agwere mʼdzenje kuti awonongedwe.
Pamenepo moyo wanga udzakondwera mwa Yehova
    ndi kusangalala ndi chipulumutso chake.
10 Thupi langa lidzafuwula mokondwera,
    “Ndani angafanane nanu Yehova?
Mumalanditsa osauka kwa amene ali ndi mphamvu zambiri,
    osauka ndi osowa kwa iwo amene amawalanda.”

11 Mboni zopanda chisoni zinayimirira,
    zinandifunsa zinthu zimene sindikuzidziwa.
12 Iwo anandibwezera zoyipa pa zabwino
    ndipo anasiya moyo wanga pa chisoni.
13 Koma pamene iwo ankadwala, ine ndinavala chiguduli
    ndi kudzichepetsa ndekha posala zakudya.
Pamene mapemphero anga anabwerera kwa ine osayankhidwa,
14     ndinayendayenda ndi kulira maliro,
    kumulira ngati bwenzi langa kapena mʼbale wanga.
Ndinaweramitsa mutu wanga mosweka mtima
    kukhala ngati ndikulira amayi anga.
15 Koma pamene ndinaphunthwa, iwo anasonkhana mosangalala;
    ondithira nkhondo anasonkhana kutsutsana nane, ineyo osadziwa.
    Iwo sanasiye kundiyankhulira mawu onyoza.
16 Monga anthu osapembedza, iwo anandinyoza mwachipongwe;
    anandikukutira mano awo.
17 Ambuye, mpaka liti mudzakhala mukungoyangʼana?
    Landitsani moyo wanga ku chiwonongeko chawo,
    moyo wanga wopambana ku mikango.
18 Ndidzakuyamikani mu msonkhano waukulu;
    pakati pa gulu lalikulu la anthu ndidzakutamandani.

19 Musalole adani anga onyenga
    akondwere chifukwa cha masautso anga;
musalole kuti amene amadana nane popanda chifukwa
    andiyangʼane chamʼmbali mondinyoza.
20 Iwowo sayankhula mwamtendere,
    koma amaganizira zonamizira
    iwo amene amakhala mwabata mʼdziko.
21 Iwo amandiseka mofuwula ndipo amati, “Haa! Haa!
    Ndipo ndi maso athuwa ife taziona.”

22 Yehova mwaona zimenezi; musakhale chete.
    Ambuye musakhale kutali ndi ine.
23 Dzukani, ndipo nyamukani kunditeteza!
    Mulimbane nawo chifukwa cha ine, Mulungu wanga ndi Ambuye anga.
24 Onetsani kusalakwa kwanga mwa chilungamo chanu, Inu Yehova Mulungu wanga.
    Musalole kuti akondwere chifukwa cha mavuto anga.
25 Musalole kuti aganize kuti, “Amati atani, zachitika monga momwe timafunira!”
    Kapena kunena kuti, “Tamutha ameneyu basi.”

26 Onse amene amakondwera ndi masautso anga
    achite manyazi ndi kusokonezeka.
Onse amene amadzikweza kufuna kundipambana,
    avekedwe manyazi ndi mnyozo ngati zovala.
27 Koma amene amakondwera chifukwa chakuti ndine wosalakwa,
    afuwule mwachimwemwe ndi chisangalalo.
Nthawi zonse azinena kuti, “Yehova akwezeke,
    Iye amene amakondwera ndi kupeza bwino kwa mtumiki wake.”
28 Pakamwa panga padzayankhula za chilungamo chanu
    ndi za matamando anu tsiku lonse.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide, mtumiki wa Yehova.

36 Uthenga uli mu mtima mwanga
    wonena za kuchimwa kwa munthu woyipa:
Mu mtima mwake
    mulibe kuopa Mulungu.